Eunice Kholowa

Eunice Kholowa Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Eunice Kholowa, Digital creator, Blantyre.
(1)

02/06/2026

Mutaonera modekha mwaphunzirapo chani?
for lesson purposes

Lero 07:00pm exactly TIKUYAMBA training yathu ndipo tiyamba ndi Hair Shampoo.Abale anuwo alipiliren...K15,000 only inuso...
02/06/2026

Lero 07:00pm exactly TIKUYAMBA training yathu ndipo tiyamba ndi Hair Shampoo.

Abale anuwo alipiliren...K15,000 only inuso ndi less than K50,000 m***a kuyamba business ya glycerin kapena shampoo nzotheka.

Surf ndamene amafunako kampamba kakakulu koma zinazi m***a kupanga inu....0881581036

Help me wishing Monica Khombe a Happy birthday🥳🥳Munthu ozichepetsa...she is the University of Malawi's Head of Marketing...
02/06/2026

Help me wishing Monica Khombe a Happy birthday🥳🥳

Munthu ozichepetsa...she is the University of Malawi's Head of Marketing and Communications koma amacheza ndaliyese...

I don't regret meeting her and aliyese anachezapo naye can attest simunthu wamba ...so supportive,humble and friendly..

May God bless you Mokho😘

Amakhala atopa, ogula akusowa, kunyumba kulibe kanthu, mkazi ndi mwana akudikira adad ali kosaka...pena agwide ndi a for...
02/06/2026

Amakhala atopa, ogula akusowa, kunyumba kulibe kanthu, mkazi ndi mwana akudikira adad ali kosaka...pena agwide ndi a forest awalandeso ...ogulawo akati anenelereso💔

Mulungu ayendereni anthu awawa ndikuwapatsa zochita zokhazikika mdzina la Yesu 🔥

Sikufuna koma mavuto 💔

Aliyese akugobola ganyu opweteka kwambiriyi Mulungu amuyendere mdzina la Yesu 🔥 Kwakwana🔥

EYA MUMAFUNA NYENGO ZANU ZITASINTHA KUCHOKA MUUMPHAWI KUTI MUKHALE OLEMERAWHAT ARE YOU DOING KUTI NYENGOZO ZISINTHE?1. C...
01/06/2026

EYA MUMAFUNA NYENGO ZANU ZITASINTHA KUCHOKA MUUMPHAWI KUTI MUKHALE OLEMERA

WHAT ARE YOU DOING KUTI NYENGOZO ZISINTHE?

1. CHIKHULUPILIRO NDI MAPEMPHERO?
Izi pazokha sizingakusinthireni nyengo.Chikhulupiliro chopanda ntchito chili chabe.Malilime sabweza ngongole nchifukwa chake tili ndi akhristu ambili osauka azibusa opemphetsa anthu omwe amati Mulungu achita iwo ali aulesi nyengo zomvetsa chisoni nkumamutukwanitsa nazo Mulungu.

Abwana aja amandida ehh nchifukwa chake sakundikweza amakondera munthu wosapemphera uja....osapempherayo amalawilira kuntchito,akafika amagwira ntchito ndipo amapanga deliver zoyenera iweyo wamalilime ukafika kuntchito phee pa TikTok, kuchedwa mkati delivery zero amukweza ndani?

You are not even willing to learn from others koma malilime omanga kuponderezedwa chonsecho performance zero nkumadana ndi anzako osapemphera aja nkumati anakulodza zazii...
Osapempherayo akadzudzulidwa amakonza palakwika...born again akalakwiridwa amasala kudya nkumaika ma status amilandu nkumamanga ziwanda vuto aliyekha.

Akati agundike kuzibakira ...ODALA OSAUKA MUUZIMU...inu umphawi ndi omwe ukupangitsa akhristu kuyamba umbava,kulowa mungongole, kuyamba zachinyengo, kuyamba uhule ...titamakhala ndixokwanira titha kumapemphera mozikhutula nkumathandiza ntchito ya Mulungu kupita chitsogolo osati kumakhala akapolo inu tisamanamizane..a born again ena anatenga matenda kamba ka umphawi...

NGAKHALE MULUNGU MWINI AMAFUNA TILEMERE,TIZISAMBA,TIZITCHENA NDIPO TIZIDYA BWINO...UKULU WAMULUNGU UZIONEKA MWAIFE ...Instead anthu osakhulupilira Mulunguwo ndi omwe akulemera.

2. BUSINESS?
Mmapanga business yanji? Business yanuyo ikupanga solve vuto lakwanuko? Olo mutatsegula hardware yapamwamba kumalo oti kuli anthu omwe akusowa zakudya muzakhalabe mmphawi...gulitsani zomwe zikufunika kwanuko...lawililani eya pangani deliver zoyenera

Mumatsatsa motani business yanu? Chomwe chingamupangitse munthu kukugulani inuyo osati anzanu aja nchani?

Ehh amene uja ngotamba amagwiritsa ntchito mankhwala...zaumve zanuzo mumati azikugulani ndani?
Zosakoma ngati zimenezo anthu azikugulirani kukumverani chisoni?

Munthu osatha kucheza ndi makasitomala ngati iwe anthu azikugulira kusimidwa? Matama thoo koma ukufuna kupanga ndalama..ndalamazodi muzimvera fungo...

Musanapite kwa abusa kuti akumangileni ziwanda muzilangize Kaye ...nawo azibusa ena kusowa zochita tamawauzani anthu zilungamo za business management asamakutopetseni...munthu akugulitsa zosakhala bwino aanthu amugula bwa?.

3. NTCHITO?
Mumapanga deliver chani? Mumagwira ntchito motani? Abwana amakudalirani? Mumalawilira?
Enanu kuntchito mmapita mochedwa, performance zero mpaka imvi position yomweyo mwano ndikutamba thoo kumangolimbana ndi abwana...how differ are u from others to deserve promotion???

4.MAGANYU?
Kuganyu kwanuko mumalimbikira motani? Munthu wamwano ngati enanu mupangidwa bwanji promote? Ulesi, mabodza kulimbana ndi abwana konseko mukufuna zanu ziyende? Mukapeza ndalamayo mmapanga nayo cha? Mukusungapo ndalama Ina yake kuti muzayambire business? Ganyu wanuyo akhale njira yopezera Mpamba osayalako mphasa sikwanu... gwirani ganyu kwakanthawi kochepa kasambeni zanu

5. ULIMI?
Mukulima cha? Zomwe mukulimazo nxopindulitsa? Kapena mungolima for fun? Mukugulitsa motani? Pano xomagulitsa raw products zinatha pezanj njira yosinthira zanuzo kuti muyambe kupanga PHINDU...zomatu ndalima matumba 100 ndipeza PHINDU ukhaula...pangani njira yosinthira matumba 100 anuwo kukhala pangolin wandalama zambili... innovation...

WAMAKANI MUMUMVA AKUZIBAKIRA UMPHAWI WAKE WANZERU AYAMBA KUSINTHA PA POST YOMWEYI.

Eyatu gulan ma pdf anga kuti Mupindule kwambiri...

01/06/2026

Ine ndapanga kwatsala inu kupanga chisankho chozaphunzira🔥🔥

01/06/2026

Ukhale mwezi wazisomo ndikukonderedwa pamoyo wanu ndi business yanu mdzina la Yesu.Zabwino zikuchitikireni.

FROM WAGANYU OMANGA ANTHU TO AN EMPLOYER AND OWNER OF 3 SALONSFrom my call ...ndalemba zomwe amayankhulaEunice do u reme...
31/05/2026

FROM WAGANYU OMANGA ANTHU TO AN EMPLOYER AND OWNER OF 3 SALONS

From my call ...ndalemba zomwe amayankhula

Eunice do u remember ndinakumana nawe kuchirimba ndinali mushop ya nzanga ndinkam***andiza nzanga kumanga tsitsi munthu and tikucheza unandiuza nditha kuyamba za mobile saloon since ndilibe ndalama zoyambira saloon?

Inetu ndinakumva ndipo ndinayamba kumayenda ndikumajambula anthu ankandiitana akaona ndapanga post pa status,pa Facebook ndi TikTok. Mu 2024 December ndinayamba kugula zipangizo zanga ndipo 2025 March ndinayamba saloon yanga pano ndili ndi ma saloon atatu and ya mobile sindinasiye mpaka tikumaitanidwa kukamanga anthu mmaukwati ndi ma event ena.

Nthawi imene ija ndinalibe kanthu ndinaphunzira kusunga ndalama chifukwa cha upangiri wako Eunice.Ndalemba anthu ntchito imagine chifukwa chaiwe and panopo am opening a classic cosmetic shop in September ku Lilongwe uzabwere.

I realized NDINGATHE ndipo ndikuthandi pano.Zikomo pondithandixa kuti nyengo zanga zisinthe.Makolo anga samvetsaso chisoni pano ndipo zoti nzayenderapo galimoto sindinkalota.May God bless u richly.

Family, I remember I met this girl mu March 2024 koma Mulungu amasinthandi munthu .....
Student akuyendera galimoto Ine ndikuyendabe ngati chiweto😅😅

Congratulations...from waganyu othandiza kumanga anthu to the owner of saloons and classic cosmetic shop and employer 🔥🔥🔥

NDI MONTH END ANU ANTHU ALANDIRA TAMUPANGENI TAG NZANU UJA AKULIPILIRENI TRAINING IYIYI MUYAMBE KUPANGA BUSINESS...IMAGI...
31/05/2026

NDI MONTH END ANU ANTHU ALANDIRA TAMUPANGENI TAG NZANU UJA AKULIPILIRENI TRAINING IYIYI MUYAMBE KUPANGA BUSINESS...

IMAGINE KUKUONETSANI INEYO NDIKUPANGA ZINTHUZO MUCHICHEWA,NKUKUPATSANI MAVIDEOWO, NKUTUMIZASO AUDIO KENAKO BUKU PA MTENGO WA 15,000 MA PRODUCT ONSE ATATU.....

NKUZAKUUZANISO KOMWE MUNGAGULE MATERIALS..UBWINO UPOSE APAPA?
TAWAFUSEN OMWE ANAJOINA SESSION YOYAMBA MUMVE MAUMBONI...CHABWINO MUONE KU COMMENT ZOMWE ZABWERA NGATI ASSIGNMENT...

0881581036 ZAJOINENI INE NSANJE NDILIBE

From inbox Pepani pokusokonezi sister koma munthune ndalemedwa mu mtimamu. Kodi makolo amene sakondwa ukafuna kuyamba zi...
31/05/2026

From inbox

Pepani pokusokonezi sister koma munthune ndalemedwa mu mtimamu. Kodi makolo amene sakondwa ukafuna kuyamba zinthu zina like ma business, ulimi kapena ndinene kuti makolo amene amakupondereza mu zinthu ngati izo koma chonsecho umphawi ukuwonekabe.

Mumapanga bwanji kuthana ndi vuto ili kapena ndingatani kuti ndithawe vuto chifukwa zimandipatsa ukali wawukulu woti sindimafunaso kukhala chifupi ngakhale ndi m'bale wanga yemwe.

Tithandizekoni maganizo

Akuti muwathandizeko maganizo awa ...

Address

Blantyre

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Eunice Kholowa posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Eunice Kholowa:

Share