Scoch news

Scoch news Scoch news company

*Nkhani yomwe yakungochitika kumene*```◽Minibus yomwe nambala yake ndi CK 8916 yachita ngozi mu msewu wa Masauko Chipemb...
17/05/2025

*Nkhani yomwe yakungochitika kumene*

```◽Minibus yomwe nambala yake ndi CK 8916 yachita ngozi mu msewu wa Masauko Chipembere pafupi ndi roundabout ya Clocktower ku Blantyre.

Minibus yi ananyamula anthu kuchoka ku Limbe kupita nawo ku Blantyre.

Malingana ndi dalaivala wa galimotoyi Edwell kuyokwa, ngoziyi yachitika pomwe galimotoyi inamasuka mabureki ndipo posafuna kuwomba galimoto zina ndipomwe inasempha msewu.

Kuyokwa wati galimotoyi inanyamula anthu 15 ndipo palimbe wamwalira.

Padakali pano apolisi afika pa malowa ndipo atengera anthu asanu ku chipatala.```

17/05/2025

*Apolisi ku Chikwawa ati adakasaka dalaivala yemwe adagunda ndi kupha bambo yemwe sakudziwika pafupi ndi msika wa Ngabu m'mawa wa lachiwiri.*

```◽M'neneri wa apolisi m'bomali, Sergeant Dickson Matemba, wauza Zodiak Online lero kuti yemwe anachita ngoziyo sanabwere poyera.

Malinga ndi Sergeant Matemba dalaivalayo adawomba bamboyu mu msewu ochokera ku Nsanje kupita ku Blantyre wa M1 koma sadayime kuti amutengere ku chipatala kuti apulumutse moyo wake.

Iye wati dalaivalayo akamupeza adzayankha milandu itatu; okupha munthu kaamba koyendetsa galimoto mosasamala, osapereka lipoti la ngozi m'maola 24 ndi kulephera kuthandiza munthu yemwe adamuwomba.

Padakalipano Sergeant Dickson Matemba wati thupi la bamboyu lidakali ku chipatala cha Ngabu ponena kuti abale ake sanadziwike.
```

*Mfumu Somanje Makata yaku Ndirande munzinda wa Blantyre yapempha atsogoleri andale mdera lake kuti akhale patsogolo pol...
17/05/2025

*Mfumu Somanje Makata yaku Ndirande munzinda wa Blantyre yapempha atsogoleri andale mdera lake kuti akhale patsogolo polimbikitsa bata ndi mtendere munyengo yokopa anthu kuti adzawavotere pazisankho zapa 16 September chaka chino.*

```◽Iwo apereka pempholi pa msonkhano umene bungwe la National Initiative for Civic Education (NICE) lidachititsa mderali pofuna kupempha anthu kupewa ziwawa pomwe dziko lino likukonzekera chisankho.

A Makata anati kwa nthawi yayitali atsogoleri a ndale akhala akugwiritsa ntchito achinyamata kukwaniritsa zolinga zawo zoyipa pa ndale, zomwe ndi zosemphana ndi malamulo a dziko lino pa nkhani ya chisankho.```

*Madandaulo okwana 200 okhuza kuphwanya ufulu wa ogula ndi omwe bungwe la Competition and Fair Trading Commission (CFTC)...
17/05/2025

*Madandaulo okwana 200 okhuza kuphwanya ufulu wa ogula ndi omwe bungwe la Competition and Fair Trading Commission (CFTC) lalandira mu miyezi itatu ya pakati pa January ndi March chaka chino.*

```◽Mneneri wa bungweli Innocent Helema wauza Mzati kuti chiwerengero cha madandaulowa ndi chokwera poyelekedza ndi chaka chatha munthawi ngati yomweyi pomwe bungwe lawo linalandira madandaulo 123.

Iwo ati mwa madandaulo omwe alandira chaka chino, ambiri ndiokhuza kukweza mitengo ya katundu mopyola ndipo otsatira ndi okhuza kusalora kubweza katungu yemwe ndi owonongeka.

A Helema ati kuchuluka kwa madandaulowa zikusonyeza kuti anthu ayamba kumvetsetsa nkhani yokhuza ufulu wa anthu ogula komanso kuti anthu akulikhulupilira bungwe lawo momwe likugwilira ntchito zake.

Bungwe la CFTC limayang'anira mipikitsano ndi kusakondera pa malonda pomwe mwazina limaonetsatsa kuti anthu sakuphwanyilidwa ufulu wawo pogula katundu.
```

17/05/2025
*🇲🇼Yemwe adali mtsogoleri wachipani cha Democratic Peoples Congress (Depeco) a Chris Daza wati adasowa kolowera mchaka c...
17/05/2025

*🇲🇼Yemwe adali mtsogoleri wachipani cha Democratic Peoples Congress (Depeco) a Chris Daza wati adasowa kolowera mchaka cha 2014 pomwe chipani cha Peoples (PP) chidatuluka m'boma ndipo mchifukwa chake adayambitsa chipanichi.*

Polankhula pamsonkhano waukulu wa achinyamata otsatira chipani cha PP omwe ukuchitikira ku Lilongwe, a Daza ati pano aganiza zothetsa chipanichi ndikubwelera kuchipani cha Peoples chifukwa akuona kuti mtsogoleri wake Dr. Joyce Banda ali ndikuthekera kosinthaso zinthu mdziko lino.

Iwo ati mu mzaka ziwiri zomwe Dr. Banda adalamulira dziko lino zinthu zidasintha monga kupezeka kwa mafuta a galimoto, ndalama zakunja ndipo aMalawi atha kusimbaso lokoma ngati atawapatsanso mwayi pachisankho chikubwerachi.

*📶🛜 🇲🇼✊‼️*Omwe anapambana pamasankho achipulira kudera la kumwera kwa boma la Salima a  Madalitso Mazombwe  atenga chile...
17/05/2025

*📶🛜 🇲🇼✊‼️*

Omwe anapambana pamasankho achipulira kudera la kumwera kwa boma la Salima a Madalitso Mazombwe atenga chiletso ku bwalo la milandu pomwe chipanichi chikufuna kuti masankhowa achitekeso.

Malinga ndi a Mazombwe akulu akulu ena kuchipani akupanga izi mwadala pofuna kuti munthu yemwe chipani chikumufuna apambane.

Mazombwe wati watenga chiletsochi kaamba koti akuwona kuti akuchitilidwa khanza.

Malinga ndi chiletso chomwe world news online yawona, a Mazombwe akufuna kuti pasakhaleso chisankho china ndipo kuti iwo apitilila ndi mulanduwu kuti bwalo lamilandu litambasule bwino za nkhaniyi.

Wapampando wa chipani cha MCP mboma la Salima a Lyton Chiphoyo ati pakadali pano sadalandile chiletsochi.

*📶🛜KHANI 🇲🇼✊‼️*Anthu a m'mudzi mwa Sailesi omwe uli pansi pa mfumu yaikulu Sitola ku Machinga adandaula kaamba ka vuto l...
17/05/2025

*📶🛜KHANI 🇲🇼✊‼️*

Anthu a m'mudzi mwa Sailesi omwe uli pansi pa mfumu yaikulu Sitola ku Machinga adandaula kaamba ka vuto lakusowa kwa madzi akukhondo kuderali.

Malinga ndi mfumu Sailesi, mudzi wawo uli ndi mabanja oposa 250 koma amadalira mjigo umodzi zomwe zimachititsa kuti anthu ena adzigwiritsa ntchito madzi a mmadambo komanso mtsinje wa shire omwe ndiosatetezeka.

Polankhula pa nsonkhano wa yemwe waonetsa chidwi chopikisana nawo pa mpando wa phungu kudera la Likwenu m'boma la Machinga a Macdonald Makanjira, mfumuyi yati izi zimaika pachiopsezo miyoyo ya anthu aderali pomwe anthu ena amagwidwa ndi ng'ona mu mtsinje wa shire ndipo ena amamira mmadzi.

Koma a Mcdonald Makanjira omwe akuima ngati phungu oima payekha ati iwo aganiza zoimira ngati phungu waderali ataona mavuto ochuluka omwe anthu akukomana nawo maka pa nkhani zosowa madzi akukhondo, milatho, kulowa pansi kwa ntchito za umoyo ndi zina.

Iwo ati, akonzeka kudzathetsa mavutowa ndikuonetsetsa kuti anthu akudera la Likwenu akukhala odzidarila pachuma ndipo ati adzatukula maphunziro, ma bizinezi, ntchito za luso kwa achinyamata komanso ulimi wa nthirila omwe udzathetse njala.

 Bungwe la MANEB latsimikizira mtundu wa aMalawi kuti ma Identity Cards a ophunzira a sitandade 8 afika m'dziko muno may...
17/05/2025



Bungwe la MANEB latsimikizira mtundu wa aMalawi kuti ma Identity Cards a ophunzira a sitandade 8 afika m'dziko muno mayeso a boma asanayambike.

Mkulu wa bungweli a Dorothy Nampota ati kampani yomwe imapanga ma ID-wa yawatsimikizira kuti likamatha tsiku la lero ma ID akhala afika.

Iwo ati ngakhale kampaniyi inakumana ndi mavuto a kusowa kwa ndalama za kunja komabe yati ichita chothekera kuti ma ID-wa afike ndithu.

Masiku apitawa bungweli lidati mwina ma ID-wa atha kufika mayeso a boma a sitandade 8 atalembedwa kale, zomwe sizidalandilidwe bwino ndi makolo ambiri a ophunzira-wa.

Mayeso a boma a sitandade 8 akuyembekezeka kuyamba lachitatu mpaka lachisanu likudzali.

Address

Mpemba
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Scoch news posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share