
26/12/2024
Ngati njira imodzi yolimbikitsa umodzi pakati pazipani zandale bungwe la atolankhani la Blantyre Press Club yapempha akulu akulu azipani kuti akhazikike pofotokoza mfundo zawo osati kunyozana pomwe dziko la Malawi likupita kuchisankho chaka chamawa.
Tsogoleri wabungweri Luke Chimwaza wanena izi pomwe akonza msonkhano waukulu wapachaka omwe uchitike pa 27 December2024 m'boma la Mulanje.
"Ife atolankhani pokhala kamwa ya a Malawi tilindi udindo obweletsa pamodzi andale kuwafotokozera kuti a Malawi akufuna chitukuko osati kunyozana kotero akufunika azifotokoza m'mene azathetsere mavuto omwe anthu akukumana nawo osati kunyozana. Pa ichi tatiana azipani zosiyanasiyana kumsonkhanowu", atero a Chimwaza.
Mwambuwu ukuyembekezera kubweretsa pamodzi zipipani monga MCP, DPP, UDF, UTM, AFORD kungotchula zochepa chabe.
Mthumwi Kuchokera Ku MEC, NICE Trust Komanso Salima sugar zikhala nawonso pamsonkhanuwu.
Wolemba Happy Makhalira- Blantyre