08/01/2026
Thank you Malawi Police Service
Bwalo la Second Grade Magistrate m'boma la Thyolo lagamula abambo atatu kukakhala ku ndende kwa miyezi 84 atapezeka olakwa pa mlandu wakuba njinga ya moto ya ntundu wa King Boss ya mtengo wa K2.5 miliyoni.
Powonekera ku bwalo la milandu, oyimira boma pa mlanduwo,a Ishmael Abubast, anauza bwalo kuti pa 31 December 2025, abambo atatu omwe ndi a Moses Davis (21), a Precious Matchado (19) ndi a Justin Musilima (19) anagwirizana zobera njinga ya moto a Matias Newiri omwe amachita bizinezi ya kabaza mu nzinda wa Blantyre.
A Abubast anati: "Patsikulo a Newiri anali ali pa malo omwe amanyamulira anthu pa Chigumula [ku Blantyre] pomwe abambo atatuwo anawapeza kuti awatenge kupita nawo m'boma la Thyolo kwa sing'anga wina."
"Ndipo usanayambe ulendowo, abambo atatuwo anapereka K10 000 yomwe anagulira mafuta a njingayo pambali ponena kuti akamulipira K30 000 akakafika ku ulendowo."
Ndipo atafika pa mudzi wa Mpando m'boma la Thyolo komwe akuti ndi kwa bwenzi la a Davis, anamuuza wanjingayo kuti asiye njingayo pakhomopo, kwinako angoyenda wapansi. Zitachitika izi anthuwo akuti ananyamuka ndi wakabazayo kumapita komwe amati ndi kwa sing'angayo koma m'modzi wa akubawo anabwerera ndi kukamasula polizira njingayo ndicholinga choti ilire mosadalira makiyi.
Atakwanitsa kuliza njingayo anayimbira lamya anzake awiri ena aja kuti basi amusiye wakabazayo yekha kuti akakumane malo ena poti njinga yomwe amayifuna ayipeza.
Wakabaza atazindikira kuti njingayo yabedwa anadziwitsa apolisi aku Thyolo omwe anayamba kufufuza kufikira pomwe njingayo inapezeka ku 6 miles ku Lilongwe pa malo ochitira chipikisheni.
A mbali ya boma anapempha bwalo kuti lipereke chilango chokhwima kaamba koti akabaza ochuluka akhala akutaya miyoyo chifukwa cha mchitidwe wa anthu onga amenewo.
Woweruza milandu ku bwalolo, a Thomson Sikweya, anati anthuwa akuyeneradi kulandira chilango chachikulu chifukwa anachita kukonzekera kuti apalamule mlanduwo ndipo anaweruza kuti akakhale ku ndende ndi kugwira ntchito ya kalavulagaga kwa miyezi 84.
Atatuwo amachokera m'mudzi wa Mtunduwatha kwa T/A Nsabwe ku Thyolo komweko.
(Wolemba: Ted Likombola - Correspondent)