01/09/2025
Katsiwiri på nkhani za ndale komanso ulamuliro wabwino, a Victor Chipofya wati mabungwe ambiri omwe si a boma (NGOs) anasiya kudzudzula ndi kuphunzitsa anthu på nkhani zosiyanasiyana kuphatikizapo za ndale kamba koti anasiya kulandira thandizo kuchokera ku mayiko a kunja.
Iwo anena izi pomwe pali nkhawa yoti mabungwe komanso andale sakuwakonzekeretsa otsatira zipani kuti adzavomereze zotsatira za zisankho.
"Mabungwe ambiri sagwira ntchito chifukwa ndiyofunika kapena kuti amayikonda, koma chifukwa amapezamo cholowa. Zikanakhala bwino asiyiretu kugwira ntchito zawo chifukwa sangamagwire ntchito kamba ka ndalama. Kumeneko ndikusowa chilungamo (hypocrisy)"
Iwo ati ngakhale mabungwe komanso andale sakuwakonzekeretsa owatsatira awo, m'Malawi aliyense ayenera kuvomereza kuti mu ndale za zipani zambiri, mumakhala opambana ndi olephera.
Mwazina, a Chipofya ati ndi pofunika kuti a Malawi akondane posatengera zipani zomwe akutsatira povomereza zotsatira zachisankhochi.
"A Malawi adziwe kuti Malawi ndi m'modzi. Zisankho, atsogoleri komanso ndale zimapita. Umodzi ndi kuyanjana kwathu ngati a Malawi kutitsogolere posatengera nyengo ya zisankho," anafotokoza motero a Chipofya.
Dziko la Malawi likuyembekezera kuchititsa zisankho zapatatu, musabata ziwiri zikudzazi pa 16 September, 2025.
Wolemba-Lumbani Kazeze