Mau Amulungu ndichida Chachipulumutso

Mau Amulungu ndichida Chachipulumutso Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Mau Amulungu ndichida Chachipulumutso, Media, Thyolo district central, Blantyre.

29/05/2020

Ambuye kodi mwandiiwala
Awe anali mau anyamata wina Yemwe anapemphera mosweka mtima kwa Nuking pomudandaulira zavuto lomwe anali nalo iye anapemphera kwa nthawi yaitali km samaona kusitha chilichonse kenako anapempha ndikt Ambuye mwandiiwala pamene anangomaliza kulakhula mau amenewa anaona maso mphenya mphamvu ya Yehova kumenyana ndiyasatana apa ndipamene anazindikira kt Mulungu ali naye ndipo akuyenera kupemphera kwambiri.
Kutheka inuso muliemunyengo yotere mwapemphera mayakho sakubwela ena mwafika pozilakhulira nokha kt zoti kwa Mulungu kuli mayakho ndakaika. Km ayi musatope pakt pamene nzeru zathu zatha ndipamene za Yehova zimayambira iye amaziwa zonse zimene mwamupempha musatope pakt mayakho anu sabwelala momwe mukufunila ngati muzatopa pempherani kt mulandile zolinga zanu Ambuye akudaliseni osaiwala kupanga share

29/05/2020

Mulungu pofuna kupereka madalitso satana amakhala waziwa ndipo amayamba kutchinga dalitsowo pofuna kutchinjiliza ndie zikafika apa mphamvu ya Yehova imayamba kumenyana ndi mphamvu ya satana ndie zimafunika kupemphera kwambiri kt dalitso uja usabwezedwe ndi demoniyi popeza mokafooka muzadusidwa khalani opemphera nthawi zonse kt dalitso wanu usakuduseni ambuye akudaliseni osaiwala kupanga share kwa anzanu

28/05/2020

Kodi mukuda nkhawa kapena mwafooka kt ambuye sakukuonani km chabwino zonsezo zili choncho tazifuseni kt ndichifukwa chiyani covid 19 sikukufikirani nanga inu muli ku South Africa tazifuseni kt ndichifukwa chani mwapulumuka ku lock down yomwe inali thafu maka kusowa chakudya. Ziwani kt sikuthekela kwanu km wakumwambayo anapanga zimenezi kt choyipa chisafikire inu tiyeni pamodzi tiimbe hosana hosana Yehova Mulungu ndikunena kt ndinu oyera mwasamalira moyo wanga ambuye oziwa kudalisa akudalinseni muzina la Yesu christu

27/05/2020

Mulungu anatuma Yesu kuzatiphuzisa kt tisate njira zake kt tikapeze chipulumutso. Yesu popita naye anasiya mau akt muzichita izi kt muzindikumbukira.Kodi inu ndichani chomwe munatengako gawo kt muzimukumbukira Yesu christu. Nanga ngati simunatenge mukudikira chiyani zimakhala zomvesa chisoni munthu akapita kuchurch akt sindingaimbe nyimbo ndikalakwisa ujen andiseka.Wina ndie akt sindingalalikire mmene ndililimu uthenga wanga sungawakhuze anthu kodi iwe ndi omwe akulalikirawo mukusiyanapo chiyan?Nanga bwanji kumowa kuja supanga manyazi nanga bwanji kujuga kuja supanga manyazi nanga bwanji kusokhano wandale kuja supanga manyazi Zimvere chisoni mbale mlongo kt ukuchedwa chifukwa nthawi ikazatha uzalira ndikukuta mano atakupasa timafuso ochepa chabe sikhasikha zamoyo wako kt ukazatha moyo uno uzaone kuwala kwa Yehova Mulungu ambuye akudaliseni osaiwala kupanga share kwa azanu

25/05/2020

Ntchito iliyonse ili ndimalipiro ake. Pamene ukugwira ntchito umadikila tsiku lozalipidwa ndipo tsiku lolipidwa lija likafika, umakondwela ndipo nthawi yolipidwa ikafika bwana ndikukuuza zavuto lako ndikuludula ndalama umakhala okhumudwa chifikwa umakhala utakodza kale budget yako. Ndie mfuso kumati ngati umadulidwa malipiro ukalakwisa pa ntchito nanga katundu wamachimo wamusenzayo patsiku lozabwela ambuye suzakhumudwa naye nanga sunazalakalaka atabwelatso tsiku lina kt ulape kaye? Abale ndi alongo nthawi sili mbari yathu ndipo ngati ukuzinamiza kt uzalapa mmawa ukuzinamiza chifukwa uzakhumudwa atate akuzatenga moyo wako munthawi yomwe sumaiyembekezera ndie khalani osamala kuopa kt mungazadandaule mutasala ndikatchimo kochepa chabe ambuye akudalinseni osaiwala kupanga share kt anebawo awone nawo.

24/05/2020

Mukuti Munalandila Yesu nanga phone number munalemba kt cousin yo ikutanimo muphone mwanumo
Mukiti Munalandila Yesu nanga make up yo mukupangilabe chiyani
Mukuti munalandila Yesu nanga miniskirt yo mukuvaliranji
Mukuti munalandila Yesu nanga jugayo mukuyendelanji
Mukuti munalandila Yesu mowa ndi fodyayo bwanji
Mukt munalandila Yesu namisecheyo
Ngati walandila Yesu khala osamala ndizitchito zako zoipazo pakt Yesu amafuna kt usiye ntchito zonse zamudima ndikuyamba ntchito zakuwala ambuye akudaliseni pamene mukusiya ntchito zanu zoipa ndikubwelela kwa Yesu mukhale ndi usiku okoma osaiwala kupembeza Mulungu musagona

24/05/2020

Ukapita kuchipata ndikupezeka ndimatenda a HIV and AIDS amakupasa malamulo ayenela kuchita kt moyo wako uziyenda bwino ndipo amatiuzatso pomwepo kt ngati simusata malamulawa moyenela muzadzaluza moyo wanu. Ndichimodzimodzitso kwa Yehova Mulungu ukafuna kutumikila iye pakulandila Yesu kukhala mbuye ndi mpulumutsi wako zimakhala chimodzimodzi. Umalandila Malamulo ten aja ndipo amakuuza usatire malamulowa kt upulumutsidwe ngati susata uzalandila chilango Ndie tiyeni tikhale akusamala pamene tikuyenda ndi Yesu kt tisalandire chilango pamoyo wathu ambuye akudaliseni osaiwala kupanga share anzanu awerenge nawo ambuye akudaliseni

23/05/2020

Yehova akamafuna kudalitsa amayamba wakupasa mayeselo kaye cholinga awone ngat ungagwe nawo ndie nthawi imeneyi imafunika kusamala kwambiri coz imakhala yowawa kwambiri chofukwa umaona ngat Ambuye akuiwala km amakhala akukuona munthawiyi chomwe amakupasa ndichitetezo basi km ukangoti waoloka mayeselo ako umazakhala mfulu mpaka kale ndie muchedwelanji kumulandila Yesu kukhala Mbuye ndi Mpulumutsi wanu landilani Yesu lero kt maplani anu atheke Mukhale ndi usiku opambana osaiwala kupanga share kt azanu wlawerengeso

22/05/2020

Kulandila Yesu sichithu chophweka zimafunika kulimba mtima kuziiwala chifukwa ndie umalandila chitozo km pamapeto ake umazapambana ndie chonde khalani olimba mtima pamene munavomereza kulandila Yesu kukhala mbuye ndipulumutsi wanu ambuye akudalinse osaiwala kupemphela musanagone kt ambuye akutetezeni

22/05/2020

Pamene mtendere wasowa pakati pako aliyense ndikumakuda kukhala olakwika umakhala dalitso uli pafupi.Kumbukilani ana aisrael pamene amakumana ndimavuto ochuluka anali atasala pang'ono kufika ku kenani choncho khalani olimba ndichikhulupiliro chifukwa chipulumutso chanu chimakhala chakozedwa kale ambuye akudalinseni nonse

16/05/2020

Watizuza kwa nthawi yaitali satana ino ndi nthawi yoti awonekele ng'amba ndie chofunika ndikugwadwa pasi kupemphere mosweka mtima kt Yehova atumize chimoto ndikumunyekesa ino ndie nthawi yake yomwe tikukhala pakhomo ukulu wamulungu ukuyeneleka kuonekela pa ife kt satana agonje tiyeni tipemphere molimbika ndikusiya utchimo wonse kt demon awoneke ng'amba

16/05/2020

Ndikupasani mtendere wanga ndikusiilani mtendere wanga mtendere omwe ndikuupereka kwa inu mukagawire kudziko konse
Awatu anali mau ambuye Yesu kuwauza ophuzira ake kt akagawe mtendere kudziko nawo ophuzira popita kumwamba anawasiyilaso ena kt apitilize kugawa mtenderewu mfuso kumati kodi inu ndi ine tikugawa mtendere kudziko kapena ayi ngati sitikugawa mtenderewu ati agawe ndindani popeza ntchito ya ambuye ndiyambiri km antchito ndiochepa ndizomvesa chisoni pazamulungu kumapanga manyazi km pamowa ndie kumasuka koopya tiyeni tizifunse kt kodi mtendere wa Mulungu ati agawe ndani ngati ine sinditengapo mbari ambuye akudaliseni usiku wabwino

Address

Thyolo District Central
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mau Amulungu ndichida Chachipulumutso posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category