23/01/2026
DZIKO LA AMERICA LASIYA KUTHANDIZA BUNGWE LA ZA UMOYO PA DZIKO LONSE (WOLD HEALTH ORGANISATION)
Dziko la United States of America(US) tsopano mwalamulo lachoka mu bungwe la za umoyo padziko lonse la World Health Organization (WHO), kukwaniritsa khumbo la mtsogoleri wadzikolo a Donald Trump omwe akhala akufunitsitsa kutuluka mu bungweli kwa nthawi yaitali.
Izi zikutanthauza kuti dziko la America lathetsa ndalama zonse zomwe linkathandiza bungweli, ndipo labweza antchito ake onse, komanso yasiya kutenga nawo mbali mu makomiti ndi utsogoleri wa bungweli.
Akuluakulu a dziko la America akuti dzikolo silinkalandira phindu loyenera pa ndalama ndi antchito amene linkapereka.
iwo awonjedzera ponena kuti bungweli lidalephera kuthana bwino ndi mliri wa Covid-19, kuphatikizapo kuchedwa kulengeza ngozi za umoyo padziko lonse komanso kudalira thandizo kuchokera ku China mliriyo pomwe mliriwo unkayamba.
Iwo akuti chisankhochi chidzalola US kupanga ndondomeko zake zaumoyo popanda kuwongoleredwa ndi mabungwe akunja amene alibe udindo wolongosoka.
Komabe, akatswiri a zaumoyo padziko lonse akuchenjeza kuti kuchoka kwa US ku bungweli ndi kuphwanya mgwirizano wapadziko lonse, kuchepetsa kupezeka kwa deta yofunika, komanso kuyika dziko lonse pangozi ya miliri mtsogolo.