10/01/2026
Mmodzi wa ochita malonda m'boma la Kasungu, a Noah Suzgo Nhlane, walimbikitsa asungwana osewera masewera a mpira wa miyendo m'bomali kuti alimbikire maphunziro komanso kupewa m'chitidwe ogonana adakali achichipere.
A Nhlane, ayankhula izi pomwe amapereka mipira kwa ma timu a Creck Ladies komanso FC Liano, pa bwalo masewero la sukulu ya pulayimale ya Chithiba.
"Tikuwalimbikitsa asungwanawa kuti alimbikire sukulu komanso kupewa m'chitidwe ogonana adakali achipere kuti akwanilitse masomphenya awo ngati Temwa Chawinga komanso Tabitha Chawinga," atero a Nhlane.
Mmawu ake, wapampando wa masewera a mpira wa miyendo m'bomali, a Moffat Time, wayamikira a Nhlane kaamba kowalimbikitsa asungwanawa komanso popereka mipira ponena kuti zithandizira kuti asungwanawa azikhala otanganidwa ndi kuzikonzekeretsa za tsogolo lawo.
Pamapeto pa mwambowu, ma timuwa anapimana mphamvu ndipo timu ya Creck Ladies, ndiyomwe inapambana ndi zigoli zitatu kwa chilowere.
Wolemba: Nelson Gonjani.