02/03/2025
MAM
Bungwe la Muslim Association of Malawi (MAM) lapempha Asilamu kuti agwiritse ntchito mapemphero a mwezi wa Ramadhan kupempha kwa Allah kuti achotse mavuto a za chuma omwe dziko lino likukumana nawo.
Wa pa mpando wa bungwe la MAM, His Eminence Sheikh Idrissa Muhammad, apereka pempholi mu uthenga wawo wa padera kudzera ku Radio Islam pomwe Asilamu pa dziko lonse ayamba kusala mmwezi wolemekezeka wa Ramadhan.
Sheikh Muhammad ati Amalawi akuvutika kuti apeze zofunika mmoyo wawo wa tsiku ndi tsiku kotero ndi koyenera kuti pa nthawi yosalayi,Asilamu apemphere kolimba kwa Allah kuti mavutowa athe.
Mtsogoleri wa Asilamuyu walongosolanso kuti mavutowa akhudzanso mabungwe a Chisilamu pomwe akuvutika kuti agule chakudya chogawa kwa Asilamu ovutika omwe akusala chaka chino.
Pokambapo pa nkhani za ndale, wa pa mpandoyu walimbikitsa Asilamu onse omwe ali ndi chidwi pa ndale kuti apikisane nawo mmipando yosiya siyana pa chisankho chomwe chikubwerachi.
Sheikh Muhammad ati ndi ufulu wa Mmalawi wina aliyense kuphatikizapo Asilamu kutenga gawo pa ndale ndi chifukwa chake akulimbikitsa kutero.
Iwo komabe alangiza Asilamu kuti apewe kugwiritsa ntchito chipembezo cha Chisilamu pa nkhani zandale ponena kuti mchitidwe woterewu umapeputsa chipembezochi.
Ramadhan ndi mwezi wa chisanu ndi chinayi wa Chisilamu womwe Asilamu pa dziko lonse amazipereka kwa Allah kudzera mu kusala, kupemphera komanso kulapa machimo.
Source:Radio Islam Malawi