12/10/2025
From Inbox
Please ndithandizeni maganizo
"Posachedwapa, ndakhala ndikuvutika. Zimandipweteka kuona mwana wanga wamkazi wa zaka 6 akuchitiridwa nkhanza ndi mkazi wanga watsopano tsiku lililonse, koma ndimadziona k*ti ndilibe mphamvu zomuletsa.
Nthawi iliyonse akamachitira mwana wanga wamkazi motere, amandiumiriza k*ti ndisalowelere nawo. Ndikudziwa k*ti sindine tate wabwino wa mwana wanga komabe ndimakondanso kwambiri mkazi wanga.
Amandimvetsetsa m'njira zomwe palibe wina aliyense, ngakhale mkazi wanga womwalirayo sadakwanilitsepo.
Ndakhala ndikuwapempha mobwerezabwereza ndikuchonderera banja la malemu mkazi wanga k*ti atenge mwana wanga wamkazi k*ti akakhale nawo. Ndinalonjezanso k*ti ndidzamutumizira ndalama pafupipafupi k*ti azisamalira komanso zosowa zake. Komabe, amaumirira k*ti azikhala ndi ine, ponena k*ti akuyenera kukondedwa ndi abambo ake ndipo sakufuna kumulanda.
Tsopano ndimadzimva kukhala wokanidwa. Ndakhala ndikumuchonderera mkazi wanga kangapo ngati angapeze njira yolandirira mwana wanga, koma amaumirira k*ti ndimupezere malo ena okhala chifukwa sadakonzekere kukhala naye m'nyumba imodzi mwana wangayo .
Pakadali pano ndikuvutika komanso sindikudziwa choti ndichite. Kunena zoona, sindikufuna k*taya mkazi wanga, amene amandikonda komaso amandimvetsetsa mozama chifukwa cha mwana wanga wamkazi.
Ndikudziwa k*ti ndiyenera kukhala bambo woteteza mwana wanga, koma ndiyeneranso kusangalala. . Ndine mnyamata wazaka 49 yemwe ndikufunanso kukhala ndi chibwenzi chokoma. Komanso mkaziyu ali ndi pakati( mimba yanga ) Kunena zowona, ndimamva chisoni kwambiri ndi mwana wanga, koma ndatayika kwathunthu.
Ndipange bwanj k*ti mwana wanga akhale otetezedwa kwa mkazi wanga komaso k*t ndisasiyane ndimkazi wanga
Please help me 💔😭