
11/07/2024
Timu ya Bangwe All Stars yomwe ndi yachitatu ku matimu omwe apondedwa kwambiri chiyambireni cha 2024 TNM Super League ikupita ku Lilongwe kukakoma ndi CRECK Sporting Club yomwe yayamba bwino chiloweleni mu mpikisanowu.
Bangwe yangokwanitsa kupambana masewero amodzi, kulepherana ndi anzawo masewero anayi ndi kugonja masewero asanu ndi amodzi pomwe CRECK Sporting Club yangongoja masewero amodzi, kupambana atatu komanso kulepherana ndi anzawo kasanu ndi kawiri.
Anyamata a Rodgers Yasin ali kuchigwa cha imfa pomwe Creck ikusangalala mu top 6.
zitha bwanji?