
25/06/2025
Nthambi ya amayi Ku Mpingo wa power house international ukuitana amayi onse okhala mu nzinda wa Blantyre ku msonkhano wa amayi pa 12 July 2025 Ku golden piccock Hotel.
Malingana ndi maibusa Lady Nancy Nkhoma msonkhanowu uzayamba 9 koloko ndipo udzatha 1 koloko masana.
Mutu wamsonkhanowu ndi 'kudzuka kwa Deborah' ndipo amayi omwe akalankhule
kwa amayi omwe adzasonkhane ndikuphatikizapo Justice Wezzie Kaira, Victoria Nkhoma,Gloria chikuse ena ambiri.
Mmawu awo, wapampando wa amayi ku mpingowu Mwenela Kamanga wati amayi onse ochoka kumipingo yosiyanasiyana ndi olandilidwa ku msonkhanowu ndipo kulowa ndi ulele.
A kamanga anati pambali pa mapemphero, pa tsikuli, kudzakhalanso maphunziro okhuza kuthana ndi nkhaza za m'banja, kuchita bwino pa chuma, upangili wa mabizinesi ndi kuchita bwino pa utsogoleri.
Olemba Elijah Banda