02/04/2024
Oweruza mlandu, Redson Kapindu, lero Lachiwiri nthawi ya 10 koloko m'mawa uno akuyembekezereka kupereka chigamulo ngati kuli koyenera kuti ma umboni ena okhudza mulandu wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulos Chilima abweretsedwe poyera ku bwaloli.
Oyimira mbali ya Chilima anapempha bwalo la milandu kuti akufuna nthambi ya Malawi Defence Force (MDF) ibweretse umboni osonyeza pomwe a Chilima adathandizira kuti a Zunneth Sattar alandire kontilakiti.
Koma, nthambi ya MDF inakana kupereka ma umboni-wa ponena kuti izi zitha kuyika pa chiopsezo chitetezo cha dziko lino.
Komabe oyimira mbali ya Chilima anafunitsitsabe kuti umboniwu ubweretsedwe ku bwaloli, zomwe zinapangitsa oweruza mulandu Justice Kapindu, kulamula MDF kuti imupatse umboniwo ndikuwuwunika m'chipinda chake ngati ulidi ndi kuthekera koyika pa chiopsezo chitetezo cha dziko lino.
A Chilima akuganiziridwa kuti analandira ndalama kuchokera kwa mponda-matiki Sattar ndi cholinga chofuna kuwathandizira kupeza ma kontirakiti mosavuta.
Wolemba:Che James Akwa Mandala