01/12/2025
Tikupitirira kuwafikira anthu osiyasiyana ma college ndi ma trading centre mdziko muno kuwaphunzitsa za kuopsa kosewera njuga mopitilita muyezo.
Kuwadziwitsa kuti;
▪️Njuga si ntchito, bizinesi kapena njira yopezera ndalama.
▪️ Ana onse osakwana zaka 18 saloledwa kuchita njuga.
▪️ Musatenge ngongole kapena kugulitsa katundu kuti mupeze ndalama zosewerera njuga.
▪️ Dziwani malire anu kuti mupewe kudzagwidwa ndi vuto la njuga (addiction).
▪️ Njuga za m’misewu (wachiona ndani) ndizoletsedwa.
Kudziwitsa mtundu wa aMalawi kuti Njuga ndi masewera chabe, aliyense akuyenera kudziwa malire ake.