10/03/2021
๐จ๐จ๐จ SONG LYRICS ๐จ๐จ๐จ
Song: ndulu
Artist: Grace Chinga Feat. Miracle Chinga
(VERSE 1) *Grace Chinga*
Chimawawa ngati ndulu,
Chimawotcha ngati moto,
Akayambitsa dala nkhani,
Ya mwana Ine ndilibe/
Poyamba timacheza tonse,
Pano amandipatula,
Chifukwa ndilibe banja,
Akuti ndingawalande/
Akaona Ndili chonchi,
Akuyesa mwanditaya,
Andifunsa mwachipongwe,
Mulungu wako ali kuti?
Nkati ndikawayendele,
Ndichipsinjo akandiona,
Pena kundizemba kumene,
Nayesa otembeleleka/
(CHORUS)
Mwana eeh, Mwana eeeh,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Patsenikoni mwana,
Nane ndiyamwitse,
Chitonzo chichoke,
Mtendele, ufulu,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Ndindani angandipatse mtendele,
Kuposa inuyo..
Dalitso, dalitso,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Zokhumba zanga zidziwika kwa inu,
Mbuye mundiyankhe..
Chuma eeh, chuma eeh,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Siliva ndi golide zonse nzanu
Nsinthileni nyengo...
(VERSE 2) *Grace Chinga*
Kwa amene munawapatsa chuma,
Andiyesa opanda nzeru,
Amati ndine opepela,
Waulesi ndi wopemphetsa/
Koma ndimakhulupilirabe,
Kuti zonse ndili nazo,
Kuuzimu mnalingeza,
Kale mwa ine zionekele/
Omwe akufuna inu,
Asafooke chifukwa Cha ine,
Akodwe mchozizwa chanu,
Nayamba kupembedza inu..
Ndipangileni chachi kulu,
Cha mtengo wake wapatali,
Adani akachione,
Natama dzina lanu/
(CHORUS)
Mwana eeh, Mwana eeeh,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Patsenikoni mwana,
Nane ndiyamwitse,
Chitonzo chichoke,
Mtendele, ufulu,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Ndindani angandipatse mtendele,
Kuposa inuyo..
Dalitso, dalitso,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Zokhumba zanga zidziwika kwa inu,
Mbuye mundiyankhe..
Chuma eeh, chuma eeh,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Siliva ndi golide zonse nzanu
Nsinthileni nyengo
(VERSE 3) *Miracle Chinga*
Amandi pekela nkhani,
Mboni zambili zonama,
Kundisowetsa mtendele,
Kundidetsela mbili yanga/
Nkati ndiyangโane uku
Nkhani ingo khala yanga,
Nkapena ndidzele kwina,
Akungondi kambilana/
Nanga ine nthawile kuti,
Ndifuna nane mpumulo,
Kapena ndipinde manja,
Kapena ndiwa tambasule/
Ndidziwa ufulu wanga,
Weni weni Uli kumwamba,
Kumene ndilindilira,
Mpulumutsi mbuye yesu...
(CHORUS)
Mwana eeh, Mwana eeeh,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Patsenikoni mwana,
Nane ndiyamwitse,
Chitonzo chichoke,
Mtendele, ufulu,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Ndindani angandipatse mtendele,
Kuposa inuyo..
Dalitso, dalitso,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Zokhumba zanga zidziwika kwa inu,
Mbuye mundiyankhe..
Chuma eeh, chuma eeh,
Nanenso mbuye ndimafuna,
Siliva ndi golide zonse nzanu
Nsinthileni nyengo.
To be continued......................................
Kwa amene amafuna ma lyrics aja ndi amenewa. Ndayambapo kupanga post.
Amene mwagula kale album, ndidzikutumizilani ma lyrics ake pa WhatsApp mwa ulele.
Amene simunagulebe album ya yotchedwa m***a kugula tsopano.
Album yi muli Nyimbo 12 za tsopano zokhazokha zoti simunazimvepo.
Ndalama yogulira album yonse ikumakhala yosachepela k2000 Ndipo kugula nyimbo imodzi ndi k500 basi.
0995304377 (airtel money)
0887329169 (mpamba)
1006621569 (NB MO626)
Mukatumiza tidzikutumizilani nyimbozi
Zikomo