Malawi Intergrated News - MIN

Malawi Intergrated News - MIN Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Malawi Intergrated News - MIN, Media/News Company, Blantyre.

Tsogolo lowala lija. Soldiers in one picture.😭😭😭
01/07/2024

Tsogolo lowala lija. Soldiers in one picture.😭😭😭

30/04/2024

Inside Our Mail-box Help a Friend

Post this for me

Ndine mzibambo wa zaka pafupifupi forty. Zikuoneka kuti ndili ndi vuto la ubereki. Ndanyenga akazi ochuluka ndithu koma palibe olo mmodzi ndinamupatsako mimba. Ndamwa zimankhwala zosiyanasiyana koma palibe kusintha. Ngati alipo wodziwa zisamba za mphamvu zoti nditha kumwa mkupereka mimba can let me know. Koma asangokhala woyesa zida chabe. Ndaberedwa kwa nthawi yayitali. Ena m***a kumati pitani kumapemphero or ku chipatala aaaa zonsezo ndinayesa ndithu koma sizinathekebe.

30/04/2024

Thanks for being a top engager and making it on to my weekly engagement list! Mac Suzex M Chaona, Owen Precious Japhet, Richard Msachi, Patrick Nantibule Banda, Yusuf Mwachikumba, Felix Thomas

27/04/2024

Super League update
FCB 2: 1 Baka Geoffrey Mwakayembe 13'| for Baka, 20'|Ephraim Kondowe, 42'|Chawanangwa Gumbo for FCB.

27/04/2024

SUPER LEAGUE UPDATE
FCB 1 : 1 BAKA goal from Ephraim Kondowe for Bullets 20'|

27/04/2024

TNM SUPER LEAGUE UPDATE
13'|Geoffrey Mwakayembe FCB 0 : 1 Baka City

27/04/2024

ABALE MTAMBO WATULUKIRANSOTU UKU

Mtsogoleri wa Citizen for Transformation (CFT), Timothy Mtambo lero adapangitsa msonkhano wa atolankhani pomwe wafotokoza kuti dziko la Malawi lili mu umphawi wadzaoneni ngakhale zaka zinayi zadutsa tili mu ulamuliro wa Tonse Alliance omwe anthu ambiri m'dziko muno adali nawo chiyembekezo kuti usintha zinthu.

Mmene zilirimu zikusonyeza kuti Mtambo atha kuyambiranso kufuna kumenyera anthu ufulu ngati momwe adachitira mmbuyomu.

Inu muti naye bwanji Timothy Mtambo yu? Ayambirenso yake ija ya mademo ija? Kapena asayerekeze kutero?

Wolemba: Davide wa ku Mangochi.

27/04/2024

Zigawenga zaba ndalama zomwe pakadali pano sizikudziwika kuti mzochuluka motani m'bandakucha wa lero pa malo omwetsera mafuta agalimoto a Total yomwe ili pafupi ndi bwalo la ndege la Kamuzu ku Lilongwe.

Omwe anawona izi zikuchitika atiuza kuti zigawengazi zisanabe ndalama, zidamenya komanso kuvulaza kaye alonda ndi ogwira ntchito ena a pamalopa.

Ofalitsa nkhani za apolisi ku Lumbadzi a Felix Kwinyani naye watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti akhazikitsa kafukufuku oti agwire mbavazi.

Wolemba: Davide wa ku Mangochi

Ulipolipo weekend yi. Gulani ticket yanu pa mpamba.
26/04/2024

Ulipolipo weekend yi. Gulani ticket yanu pa mpamba.

A Kondwani Nankhumwa ayambitsa chipani chawo. Izi zachitika patadutsa nthawi ndithu atachotsedwa mchipani cha Democratic...
26/04/2024

A Kondwani Nankhumwa ayambitsa chipani chawo. Izi zachitika patadutsa nthawi ndithu atachotsedwa mchipani cha Democratic Progressive Party. Zili ndi ife a Malawi kulowa mu chipanichi poti ndi ufulu wathu.

26/04/2024

Wophunzira wina wa folomu 4 pa sukulu ya sekondale yoyendera ya Kalenge m'boma la Chitipa wa zaka 20 wazipha pozimangilira mnyumba yomwe amakhala ku Chipwela m'bomali.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya m'boma la Chitipa a Mathews Mfune wati wophunzirayu, Justin Mulungu, amachokera m'mudzi wa Reuben m'dera la Mfumu Yaikulu Mwenemisuku m'boma lomweli la Chitipa.

A Mfune ati izi zachitika Lachitatu pa 24 April m'nthawi yakumasana.

Malingana ndi a Mfune, wodziphayu wasiya uthenga oti wazipha ati kamba koti bwenzi lake lapamtima lomwe wakhala nalo pa ubwenzi kwa nthawi yayitali lathetsa ubwenzi wawo.

Pakadali pano, apolisi m'bomali apempha anthu omwe akudutsa mu nyengo zosokoneza ubongo kuti azipeza uphungu kwa akadaulo m'malo mozipha.

Wolemba: Davide wa ku Mangochi.

Nyerere or ma pale?FCB Nyasa Big Bullets has unveiled the new jersey today while Mighty Mukuru Wanderers did the same we...
25/04/2024

Nyerere or ma pale?

FCB Nyasa Big Bullets has unveiled the new jersey today while Mighty Mukuru Wanderers did the same weeks before.

Ndiye CEO wa Bullets Suzgo Nyirenda wanenetsa kuti chaka chino kuli ukweche.

Wolemba: Davide wa ku Mangochi.

Address

Blantyre

Telephone

+265883617121

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Malawi Intergrated News - MIN posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share