03/02/2026
ECHOES OF A STRANGER
CHAPTER 3
“Hey, Melifa. Its Joe. Ndinasangalala kwambiri kugwira nawe ntchito lero. Have a lovely night.”
Kodi anatenga kuti nambala yanga? Anatenga kwa bwana anga?
Maganizo anga ankathamanga ndi malingaliro osiyanasiyana, ndipo palibe ngakhale limodzi lomwe linali londilimbikitsa mtima.
Ndinayamba kulemba uthenga oti ndimuyankhe Joe. Ndimati kulemba kenako kufufuta. M’malo mwake, ndinayimbira Tadala.
“Tadala, Joe just sent me a text,” ndidatero ndipo naye adatutumuka.
“Zoona? Tadikira… wati Joe?!” Adafusa.
Ndidamuwerengera uthengawo, ndipo naye adayamba kundifusa.
“Eeh, choyamba, anatenga kuti nambala yako? Ndipo akufuna chiyani?”
“Sindikudziwa!” ndinayankha ndikuziponya pabedi. “Izi ndi zachilendo kwambiri. Nditani?”
“Muyankheni munthu” adananena ngati kuti munthawiyi chidali chinthu chosavuta kwambiri kuchita padziko lapansi.
“Ndiyankhe kuti chani? Zikomo? Naweso ugone bwino?”
Tadala anaseka. “Komatu Melifa…. Anyway, muwuzeni kuti ‘Zikomo, inunso’ mukhale pakatikati. Osamulola adziwe kuti akukusokoneza.”
Ndinapumira m’mwamba. “Chabwino. Bola zisathere pa Mikozi”
Ndinatumiza uthengawo ndipo nthawi yomweyo ndinafundira blanket langa kuti ndizigona.
Foni yanga inalira kachiwiri.
“Bwanji, ugona mochedwa?” Ndinang’ung’udza. Zachidziwikire adali ataona nthawi.
“Mawa ndi tsiku lalikulu. Ndikungoganiza kuti project iyenda bwanji”
“I feel the same way. Ndikuyembekezera kugwira nawe ntchito kachiwiri” anayankha.
Sindinayankhe. M’malo mwake, ndinazimitsa foni nkuyisiya pansi pa pilo yanga. Ndinkangofuna zindichoke.
M’mawa wotsatira ndinanyamuka kupita ku ofesi ndikumva ngati sindinagone ngakhale pang’ono. Joe anali atafika kale atakhala patebulo pake akulemba ngati kuti sanasokoneze moyo wanga usiku wonse wadzulo.
“Good morning, Melifa,” anatero akukweza maso ake ndi kumwetulira komwe nkati mwanga kunkandikwiyitsa koma pamaso ndinkasekelera.
“Morning” ndinalankhula ndikuzemba kuphana naye maso.
Patangopita mphindi zochepa Dr. Phiri analowa akuoneka osangalala kuposa masiku onse. Adali atabwerera kuchokera kunja msanga kuposa momwe tinkayembekezera.
“Mwamvanatu anthu inu” anatero, akuyang’ana ine ndi Joe.
“Simukunama bwana. “Melifa ndi munthu wabwino kwambiri.” Joe anayankha mwansaga
Ndinazikakamiza kumwetulira koma mkati mwanga sizidandisangalatse.
Tsikuli linatha mwachangu. Ma meeting apo ndi apo komanso kusintha projekiti. Joe anali waukadaulo monga nthawi zonse, koma nthawi iliyonse maso athu akakumana, ndimamva kugunda kwa mtima wanga.
Pa nthawi ya chakudya cha masana Tadala adandikoka.
“Anakutumiziranso uthenga?” anafunsa maso ake akuyang’ana komwe kudali Joe
“Inde” ndinavomereza. “Koma sindinayankhe text yake yachiwiri.”
“unachita bwino. Ofunika kumusiya choncho” Tadala adalankhula akugwedeza mutu wake.
Pofika kumapeto kwa tsikuli ndinali wokonzeka kupita kunyumba n’kuyiwala Joe kwathunthu. Koma pamene ndinkanyamula zinthu zanga anabweranso pa desk panga.
“Melifa. Ndimangofuna kudziwa ngati ungakonde titakamwa coffee mawa m’mawa. Adatero.
Ndinazengereza. Ankandifunira za ntchito kapena zina?
“No problem” ndinayankha.
“Just coffee right?”
Joe anangomwetulira. Yes, coffee basi.” Adatero ndikumapita
Usiku watsiku limeneri ndidachezera kuwerenga malata. Kodi vuto la Joe linali chiyani? Kodi ankangofuna ticheze, kapena panali china chopitirira pamenepo?
Posakhalitsa phone yanga inalira ndipo ndinatenga mokaika.
“Hey Melifa. Ndi Joe. Can’t wait for Coffee tomorrow. Good night.”
Ndinang’ung’udza. Munthu uyu anali okakamila.
“Zikomo. Goodnight too” ndidayankha.
Ndinazimitsa foni n’kuyisiyanso pansi pa pilo yanga. Koma pamene ndinkalowa tulo, lingaliro limodzi silidachoke.
Kodi Joe akufuna chiyani kwenikweni?