
16/07/2025
CECAFA IBWENZA NDALAMA ZA MALAWI NDI SEYCHELLES
Bungwe la CECAFA lalonjeza kuti libwenza ndalama zonse zomwe matimu a mpira wapagombe a Malawi ndi Seychelles aononga pomwe anali atafika kale m'dziko la Kenya kukasewera mpikisano wa maiko a pansi pa bungweli.
Izi zachitika pomwe matimu awiriwa aomba mgolo kutsatira kuti anali atanyamuka kale Koma bungweli lasuntha masiku a mpikisanowu.
Matimu a Malawi ndi Seychelles analandira kalata yowapempha kukachita nawo mpikisano a masewero apagombe ndipo kutsatira kuti masiku anayandika, matimuwa ananyamuka kupita ku mpikisanowu.
Koma bungwe la CECAFA lapepesa ku dziko la Malawi komanso Seychelles Kamba koti uthenga wawo wakusintha masiku a mpikisanowu aufotokoza mochedwa ndipo lalonjeza kubwenza ndalama zonse zomwe awononga pa ulendowu.
Padakali pano, timu ya Malawi ikupanga zoti ibwerere m'dziko muno ndipo mphunzitsi watimuyi, W***y Kumilombe, wadandaula Kamba koti timu yake inakonzeka bwino.