24/07/2025
Bwalo la milandu la Senior Resident Magistrate ku Mangochi lalamula a Allie John a zaka 28, kuti alipire chindapusa cha ndalama zokwana K720,000 ndikuti asayendetsenso galimoto kwa chaka chimodzi kaamba kochita zinthu zosemphana ndi malamulo a pamsewu a gawo 110, 128, 18 komanso 11.
Kudzera mwa oyimira boma pa milandu, a Grace Mindozo, bwalori linamva kuti pa 25 June 2025 a John anapalamula milanduyi pomwe anapanga phokoso losowetsa mtendere pa malo ochitira malonda a pa Soko pothamangitsa galimoto lawo la mtundu wa Mazda pick-up lomwe mkatikati mwa liwiloro limamveka ngati akuwomba mfuti.
A Mindozo anauza bwalori kuti apolisi akhala akulandira madandaulo ochuluka okhudza m'chitidwewu omwe kawirikawiri umachitika nthawi ya usiku.
M'chitidwewu kupatula kusokoneza mtendere wa anthu, umasokonezanso apolisi opereka chitetezo usiku.
Kuwonjezera pa mulandu ochita phokoso lopanda pake, a John amawazenganso mulandu oyendetsa galimoto ataledzera, kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo, kuyendetsa galimoto lopanda misonkho komanso kuyendetsa galimoto popanda chiphaso.
Ku bwalori a John anavomera okha milandu yonse inayi yomwe amawazenga ndipo anapempha kuti awachitire chifundo popepesa kwa anthu okhala mu tawuni ya Mangochi komanso apolisi ponena kuti anachita zinthu zosayenera.
Koma m'chigamulo chake, senior resident magistrate Muhammad Chande analamula a John kulipira ndalama zokwana K180,000 pa mulandu uli onse zimene zonse pamodzi zikukwana K720,000 zomwe a John alipira kale.
A John amachokera m'mudzi wa Kalonga m'dera la mfumu Mponda m'boma la Mangochi.
(Wolemba: Ayamba Kandodo-Correspondent)