Timuziwe YESU Masiku Osiriza

Timuziwe YESU Masiku Osiriza kufalisa uthenga wa mulungu

25/09/2022

WORSHIP A FATHER NOT SON

03/01/2021

Mutu wa uthenga wathu wa lero ndi kusunga sabata.
Bible likutiuza bwino kuchokela mu bible kuti Mulungu atalenga zonse za padziko lapansi ndi zakumwamba adapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ndipo tsikuli adaliyelesa kuti likhale lopatulika pa Genesis 2:2-3 zitapita izi Mulungu adamulamulila Moshe kuti uzilipatula tsiku la sabata kuti likhale lopatulika pa ekisodo 20:8, izi Mulungu adamulamulila kuti tizizichita monga mene adanenela ndipo malamulo a Mulungu sadathe ndipo sazatha ayi azakhalapo mpaka chisilizilo cha dziko lino lapansi chifukwa malamulo onse adapelekedwa kwa anthu chifukwa cha uchimo wawo. Ndiye tonse amene timafuna zopulumuka tikuyenela kusata malamulo onse omwe Mulungu wathu adatilamulila kuti tizisata chifukwa pa yakobo 2:10 kuti ngati usata malamulo ena ndikusiya ena pamenepo uli chabe ndinthu pamaso pa Mulungu.yuda 1:3

03/01/2021

Okondedwa abale ndi alongo ndakulandilani nonse amene mwapanga like page iyi. Mu page iyi tizikhala ndi uthenga tsiku lililose kukamatheka. Zikomo nonse

28/12/2020

Hosea 4:6 anthu anga akuonongeka chifukwa cha kudziwa, anthu ambiri matsiku omalidza uzachulukile ndi ugothi komanso okonda kuyenda mu zilakolako za iwo eni monga mene akunenela pa 2 petro 3:3.

27/12/2020

Yohane 14:15 ngati mukonda ine sungani malamulo anga. Fuso langa nali Kodi mumamukonda Mulungu ngati mumamukonda mumasunga malamulo ake onse omwe anatilamulila monga kusunga sabata mukonda dzako mene mumazikondela inu mwini ndi ena otelo.

25/12/2020

DID YOU KNOW:Tsiku lomwe mwana wa Mulungu wa moyo anabadwa sipa 25 December ayi kwa nonse omwe mumaona ngati mwana wa Mulungu wa moyo anabadwa tsiku limeneli mumangochedwa kusiya zomwe mumapanga ndikumasangalalila tsiku ngt limeneli.kwa amene muli ndi mafuso ndifuseni

23/12/2020

DID YOU KNOW: Dzina loti Yesu ndi dzina lochita kupangidwa si dzina la mwana wa Mulungu wa moyo. Ndipo silimatathauza kuti mpulumusi ayi. Apa pamachitika zachinyengo osati masewela. Kwa amene akufuna kudziwa zambiri atha kumandifusa mafuso

22/12/2020
21/12/2020

Okondedwa abale anga ndafuna ndikudandaulileni kathu aka lero. Koyamba satana anamuononga munthu pakumunamiza kenako adamuchimwisa munda uja wa eden ndikumupangisa kuti ulemelero onse womwe adali nawo awutaye ndikuwuluza. Izi satana sanakhutile nazo kuti zomwe amafuna zatheka sadamusiye munthu koma adapitiliza kumukokela ku uchimo mpaka pamene Mulungu adakwiya naye munthu ndikumusiya manja mwa adani ake. Koma popeza munthu amamukonda munthu kwambiri adamulandisa manja mwa adani Aja ndikumulonjeza kuti amupasa dziko lolonjezedwa la mkaka ndi uchi.satana sanamusiye munthu koma adapitilizabe kumuchimwisa pamaso pa Mulungu. Messiah mpulumusi wanthu za kudzuzika kwa munthu adamuvela chisoni ndikupanga chisakho kuti amufele ndikumuyanjanisaso pamanso pa Mulungu. Koma satana sadalole kuti munthu ayanjaneso ndi Mulungu koma adayesesa kumupasa mavuto a moyo ndi milungu yosayenela cholinga azingochimwabe. Lero lino chilungamo cha Mulungu wachiyika pobisika ndicholinga choti munthu asayanjanebe ndi Mulungu. Ndikukudandaulilani yesesani kusata chilungamo chake cha Mulungu poti zambiri zimene zikuchitika matsiku ano zikumaoneka ngati zoona koma zili zaboza. Tikuyenela kuvala maso a uzimu kuti tizindikile za ichi,palibe nkhani yovuta padziko la pansi kuposa ya chipulumuso abale anga.

Address

Blantyre

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Timuziwe YESU Masiku Osiriza posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Timuziwe YESU Masiku Osiriza:

Share

Category