Blantyre Synod Radio

Blantyre Synod Radio Proclaiming The Gospel Of Our LORD JESUS CHRIST SOUTHERN REGION: 91.1FM
CENTRAL REGION : 100.3FM
NORTHERN REGION: 103.5FM
EASTERN REGION : 88.6FM

Mtsogoleri wa National Resolution for Change NRC Danis Mahata walangiza achinyamata m'dziko muno kuti asamatengeke ndi a...
15/07/2025

Mtsogoleri wa National Resolution for Change NRC Danis Mahata walangiza achinyamata m'dziko muno kuti asamatengeke ndi andale amene adzifuna kuwagwiritsa ntchito kuyambitsa ziwawa.

Mahata wauza BSR online kuti ino ndi nthawi yakuti amalawi adzimvetsera mwachidwi mfundo zimene andale akhale akufotokoza m'misonkhano yawo yokopa anthu, ndipo pamapeto pake adzapange chiganizo chabwino posakha mtsogoleri oyenera.

Mtsogoleri wa NRC'yu, wati dziko lino likufunika mtsogoleri amene adzakwanitse kukonza chuma, komanso kuti dziko lino lidzikwanitsa kukolora chakudya chokwanira .

Robert chandilira
....

Kambani a Malawi pa wailesi ya Blantyre Synod okupatsirani Emmanuel Harry komanso Jones Chizenga (07:20am - 08:00am)Chiw...
15/07/2025

Kambani a Malawi pa wailesi ya Blantyre Synod okupatsirani Emmanuel Harry komanso Jones Chizenga (07:20am - 08:00am)

Chiwerengero cha anthu omwe akufuna kuzaimira ngati mtsogoleri wa dziko lino chafika pa 18 tsopano kutsatira kubwera kwa yemwe ali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Micheal Biziwiki Usi ndi chipani chawo cha Odya Zake Alibe Mlandu.

Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) latsimikiza kuti a Usi atenga zikalata zofuna kuimira pa udindo umenewu.

Polankhulapo pa nkhaniyi, mtsogoleri wa chipani cha AFORD, Enock Chihana wati kukwera kwa chiwerengero chimenechi ndi chitsimikizo choti anthu a ndale m'dziko muno ali ndi dyera.

Chihana analankhula mawu amenewa pomwe amafika mu mzinda wa Blantyre kudzagwira ntchito za chipani chawo.

Kodi kukwera kwa chiwerengero chimenechi ndi nkhani ya dyera ngati umo walankhulira mtsogoleri wa chipani cha AFORD kapena kulikonda dziko la Malawi?

Mtsogoleri wa dziko lino,  Dr Lazarus Chakwera,  wati pasapezeke munthu wina ophwanya ufulu wanzake pamene nyengo yokopa...
14/07/2025

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wati pasapezeke munthu wina ophwanya ufulu wanzake pamene nyengo yokopa anthu pokonzekera chisankho cha pa 16 September yatsekulidwa.

Dr. Chakwera walakhula izi lolemba madzulo mu uthenga wake opita kwa amalawi okhudza nyengo yokopa anthu.

Iye wapempha amalawi kuti ateteze ufulu wawo wochita ndale omwe ndiwotetezedwa ndi malamulo.

Mtsogoleri'yu wati ngakhale kuti munthawi yokopa anthu zotonzana zimachuluka, aliyense ali ndi ufulu otsutsa zomwe zayankhulidwazo, koma munthuyo asatsekedwe pakamwa.

Dr. Chakwera watsindika kuti pasakhale munthu owopseza nzake, ndipo aliyense ateteze ufulu wosunga malamulo.

Amene amalakhulapo pa zautsogoleri Caesar Kondowe wayamikira zimene wanena mtsogoleri'yu kuti ndizothandiza pamene nyengo yokopa anthu yayamba.

Kondowe wapempha atsogoleri onse a zipani kuti akhale patsogolo kulimbikitsa owatsatira za bata ndi mtendere.

Bungwe la MEC lakhazikitsa nyengo yokopa anthu lolemba, pamene dziko lino ikuyembekezeka kukhala ndi chisankho chachikulu pa 16 September chaka chino.

.....

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera alakhula ku mtundu wa amalawi lero lolemba.Malingana ndi ofalitsa nkhani k...
14/07/2025

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera alakhula ku mtundu wa amalawi lero lolemba.

Malingana ndi ofalitsa nkhani ku nyumba ya boma Anthony Kasunda, mtsogoleri'yu alakhula kuyambira nthawi ya 7 koloko madzulo ano ndipo wailesi ndi kanema wa MBC ndi nyumba zina zoulutsa mau ziulutsa zonse.

.....

Nthambi ya Polisi yapempha zipani za ndale ndi andale kuti asamatenge nyengo ya kampeni ndi chisankho ngati nthawi ya nk...
14/07/2025

Nthambi ya Polisi yapempha zipani za ndale ndi andale kuti asamatenge nyengo ya kampeni ndi chisankho ngati nthawi ya nkhondo kapena zisokonezo chifukwa limeneli ndi gawo chabe la ulamuliro wa demokalase.

Wachiwiri kwa mkulu wa a polisi Noel Kayira ndi amene wanena izi ku Lilongwe pamwambo okhazikitsa nyengo yokopa anthu pa chisankho cha pa 16 September.

Kayira watsindika kuti apolisi adzamanga ndi kuzenga mlandu aliyense ophwanya malamulo mu nyengo yokopa anthu.

Iye wati awonetsetsa kuti malamulo onse a chisankho kuphatikizapo ndondomeko zoyendetsera kampeni zomwe bungwe la MEC lakhazikitsa lero zikugwira ntchito ndipo zikutsatidwa.

Kayira wati Polisi nayo idzapereka chilango kwa adindo, wapolisi kapena ofesala aliyense yemwe apezeke akuyambitsa kapena kulimbikitsa ziwawa ndi chisokonezo pa kagwiridwe ka ntchito yake mmalo onse a polisi.

Robert Chandilira
....

Mkulu wa nthambi yolemba zipani yotchedwa Registrar of Political Parties Kizito Tenthani walangiza mipingo mdziko muno k...
14/07/2025

Mkulu wa nthambi yolemba zipani yotchedwa Registrar of Political Parties Kizito Tenthani walangiza mipingo mdziko muno kuti isamapemphe ndalama anthu andale maka mu nyengo ino yokopa anthu pokonzekera zisankho za pa 16 September.

Tenthani walakhula izi pa mwambo otsekulira masiku ookopa anthu mu mzinda wa Lilongwe umene wakonzedwa ndi bungwe la MEC pamene pali nthambi zosiyanasiyana zokhudzidwa ndi zisankho.

Iye wati mipingo ileke kuitana andale mkumalandira ndalama zao kamba koti akhoza kuwaika m'mavuto pophwanya malamulo azisankho mu nthawi yokopa anthu.

Iye wati nthambi Yao ionetsetsa kuti lamulo ligwira ntchito pa aliyense yemwe ataphwanye malamulo a mundondomeko yakayendetsedwe ka zipani.

Mwa zina iye wati malamulo mu ndondomeko ya zipani komanso zisankho akuletsa kugawa ndalama pa nthawi yokopa anthu, kukopa anthu kumaliro komanso m’matchalitchi.

Robert Chandilira
....

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wafikanso mu mzinda Blantyre kudzera pa bwalo la ndege la Chileka pamene al...
14/07/2025

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wafikanso mu mzinda Blantyre kudzera pa bwalo la ndege la Chileka pamene ali ndi ntchito zina zaboma zokuti agwire mchigawo chakumwera.

Chakwera anali kale mu mzinda'wu koma loweluka anapita mu mzinda wa Lilongwe kukakhala nao pa mwambo wa mapemphero a mpingo wa Anglican wodzodza Ambuye Daniel Kalonga kukhala Bishop wa dayosizi ya Lake Malawi.

Pabwalo la Chileka, President Dr Chakwera walandiridwa ndi akuluakulu aboma, kuphatikizapo Nduna ya Zofalitsa Nkhani a Moses Kunkuyu ndi Nduna ya Zokopa Alendo, a Vera Kantukule, akuluakulu achipani, mafumu ndi ena.

.....

Bungwe loyendetsa zisankho m'dziko muno la MEC lati, kuti zisankho za chaka chino zikhale zovomelezeka  komanso zopamban...
14/07/2025

Bungwe loyendetsa zisankho m'dziko muno la MEC lati, kuti zisankho za chaka chino zikhale zovomelezeka komanso zopambana zikudalira aliyense kutengapo mbali .

Andrew Mpesi, wamkulu oyendetsa zisankho kubungwe'li wanena izi pamwambo otsegulira masiku makumi asanu ookopa anthu pa zisankho za pa 16 September chaka chino.

Pa mwambo'wu pabwera azitsogoleri onse azipani 24 zomwe zili mkaundula wabungwe'li, amabungwe oima paokha komanso akazembe amaiko ena.

Ben Chakhame mkulu wabungwe la Centre for Multiparty Democracy ( CMD) wati nyengo'yi sinthawi yoti zipani zikagwebane, koma kuti zipani'zi zizikatsitsa mfundo.

Chakhame wati iyi si nthawi yakuti zipani zikaonetse kuti amatha kutumiza anyamata azikwanje zakuthwa ndani, kapena kuti ali ndithanzi kuposa mzake ndani, koma akachilimike kupereka mfundo kwa amalawi.

Chakhame wati ndizomvetsa chisoni kuti nthambi zachitetezo monga a polisi ndi asilikari a MDF amatha kuonelera anthu ena akusema anthu ena ndi zikwanje, ndipo wapempha kuti ino ndi nthawi yoti akonze zovutazi.

Robert chandilira
.....

Kambani a Malawi pa wailesi ya Blantyre Synod okupatsirani Emmanuel Harry komanso Jones Chizenga (07:20am - 08:00am)Ntha...
14/07/2025

Kambani a Malawi pa wailesi ya Blantyre Synod okupatsirani Emmanuel Harry komanso Jones Chizenga (07:20am - 08:00am)

Nthambi zokhuzidwa pa nkhani ya chisankho lero pa Lolemba pa14th July 2025, zikhamukira ku Bingu International Convention Centre (BICC) mu mzinda wa Lilongwe komwe bungwe la Malawi Electoral Commission MEC likuyembekezereka kutsegulira nyengo yokopa anthu kuti azasankhe atsogoleri aku mtima kwawo pa zisankho zomwe zichitike m'dziko muno pa 16 September.

Kodi inu mukuyembekezera mawu otani ochokera ku bungwe la MEC kupita kwa onse okhuzidwa pa zisankho zimenezi?

Tiuzeni maganizo anu...

Ngati njira imodzi yopititsa patsogolo kufalitsa uthenga wabwino kudzera m'maimbidwe, Dr Matthews Ngwale amene akudzapik...
13/07/2025

Ngati njira imodzi yopititsa patsogolo kufalitsa uthenga wabwino kudzera m'maimbidwe, Dr Matthews Ngwale amene akudzapikisana nawo ngati phungu wa ku nyumba ya malamulo oyima paekha kudera la Chiradzulu Nyungwe, lamulungu wakhazikitsa mpikisano wamaimbidwe wa ma choir pa sukulu ya pulaimale ya Nyungwe m'boma'lo.

Ngwale wauza BSR online kuti mpikisano'wu wakhazikitsidwa ngati chikumbutso kukumbikira mzimu wa malemu m'busa Henry Ngwale amene anali mkulu oona za maimbidwe mu mpingo wa CCAP Blantyre Synod.

Iye anatsindika popempha ma choir amene akuyembezereka kutenga nawo mbali mu mpikisano'wu kunena kuti asunge bata komaso kuvomereza zotsatira kuti ntchito yobukitsa uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu Khristu ufalikire kutali.

M'mawu ake wachiwiri kwa wa pampando amene ayendetse mpikisano'wu, Nelia Magwede, anati ali ndichikhulupiliro kuti mpikisano'wu usintha komaso kutembenuza miyoyo ya anthu ambiri kudzera m'maimbidwe.

M'modzi mwa amene anali nawo pa mwambo'wu, Violet Joseph wa mpingo wa Namikate CCAP mu Blantyre Synod, anati mpikisano wa maimbidwe'wo wafika mu nthawi yabwino ndipo akonzekera mokwanira kuti achite bwino.

Ma choir okwana 80 azipembedzo zosiyanasiyana a m'dera la Chiradzulu Nyungwe ndi amene akuyembekezera kupikisana mu mpikisano'wu umene ndi wandalama zokwana 5 million kwacha ndipo ukuyamba kumathero kwa sabata'yi.

~ Piliran Chitekwe ~
....

Mtsogoleri wachipani ha Freedom Khumbo Kachali wati mgwirizano wa zipani za Northern Alliance ndiokonzeka kupanga m'gwir...
13/07/2025

Mtsogoleri wachipani ha Freedom Khumbo Kachali wati mgwirizano wa zipani za Northern Alliance ndiokonzeka kupanga m'gwirizano ndi chipani chomwe chidzakonze mseu ochokera ku Mzuzu kukafika ku Songwe, komanso m'godi wa Kayerekera udzipindulira Malawi, kuphatikizapo anthu aku mpoto.

Kachali walakhula izi pa bwalo la sukulu ya primary ya Baka m'boma la Karonga pa msokhano omwe zipani za mumgwirizano wa zipani'zi zinakonza.

Mtsogoleri wachipani cha NDP Frank Tumpale Mwenefumbo amene analinso pa msonkhano'wu wati anthu aku mpoto analonjezedwa bwalo landege lapamwamba, chipatala chachikulu, komanso sukulu ya ukachenjedwe, koma sizinatheke choncho m'gwirizano wawo ndioti ubweretse chitukuko'chi.

Pamsonkhano'wu panabwera atsogoleri azipani zonse zimene zili mu m'gwirizano wa zipanizi .

Robert chandilira
....

Mpingo wa African Continent Mission (ACM), womwe likulu lake lili m'dziko la South Korea, lero watsegulira tchalitchi ch...
13/07/2025

Mpingo wa African Continent Mission (ACM), womwe likulu lake lili m'dziko la South Korea, lero watsegulira tchalitchi chapamwamba cha Mvunguti ACM m'dera la mfumu yaikulu Nyezerera m'boma la Phalombe.

Nthumwi komanso Abusa a mpingowu motsogozedwa ndi akuluakulu ake ena kuno ku Malawi ndiwo anatsogolera mapemphero otsegulira tchalitchichi.

M'mawu ake m'busa Paul Chiwaula yemwe akuyan'ganira tchalitchichi wati ndiwokondwa kuti likulu la mpingowu lachitsegulira.

Chiwaula wati kumangidwa komanso maonekedwe apamwamba a mpingowu makamaka kuderali, kulimbikitsa akhristu ake kukhala olimbikira ku nkhani yamapemphero.

Tchalitchi chimenechi chili pa m'ndandanda wa nambala 151 kumangidwa pansi pa mpingowu komanso ndi thandizo lochokera ku mpingowu.

ACM ili ndi nthambi zake m'maiko onse amuno mu Africa.

Address

Blantyre

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Blantyre Synod Radio posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Blantyre Synod Radio:

Share