
08/07/2025
TABWERA KUZATENGA UKATSWIRI WA REGION 5 - JEGWE
Mphunzitsi wa timu ya dziko lino yampira wamiyendo yosapyola zaka 20, Milias Pofera Jegwe wati cholinga chake ndikutenga ukatswiri wachikho cha Region 5.
Jegwe wayankhula izi atatha masewero omwe Flames yachisodzerayi yazigulira malo mundime ya matimu anayi itagojetsa Namibia ndi zigoli ziwiri zomwe zinabwera mu gawo la chiwiri la masewerowa.
Iye wati ngakhale panali zophinja zina monga kusakhala ndi nthawi yokwanila yakakonzekeledwe komanso kupita ndi osewera 17 kumpikisanowu malo mwa 20, sizinawoneke kwambiri kamba ka ubale wabwino omwe ulipo pakati pa osewera komanso aphunzitsi atimuyi.
Malawi yamaliza pa mwamba pa group A ndi mapointi wokwana 7, pomwe Angola, ili ndi mapointi 7 kufanana ndi Flames pa nambala yachiwiri koma ikutsalira ndi zigoli pamene eni bwalo Namibia ali nambala yachitatu ndi mapointi atatu ndipo Zimbabwe ndiyomwe ili pamapeto pomwe sinapeze chipambano chilichonse.
Olemba Peter Nyasulu,Lilongwe.