The Nyasaland Post

The Nyasaland Post _International news updates
_Sports updates
_Jokes
_Entertainment
(1)

11/09/2026

Mukutitsatira kuchokera mu mzinda komanso dziko liti? From which country are you following "The Nyasaland Post". Tiuzeni ๐Ÿ˜

10/09/2026

Mtengo wa mafuta kunja wafika pa $108 โ›ฝ๐Ÿš˜ (oil price per barrel). Nkhondo ikupitilirabe pakati pa Iran ndi America. ๐Ÿ˜

10/09/2026

BREAKING NEWS: Asilikali otchedwa ma Houthis ku Yemen alandanso kachilumba kena kotchedwa Zukar Island mu nyanja ya red sea.

Sim'mene kulili ku Yemen, asilikali otchedwa ma Houthis ku Yemen alanda mzinda wa m'mphepete mwa nyanja otchedwa Al Mokh...
10/09/2026

Sim'mene kulili ku Yemen, asilikali otchedwa ma Houthis ku Yemen alanda mzinda wa m'mphepete mwa nyanja otchedwa Al Mokha (Mocha) ndipo apa akulowera penipeni pa Bab al Mandeb Strait omwe ndi malo aang'ono kwambiri mu nyanja imeneyi ya red sea pomwe sitima zambiri zimadutsapo.

Omvera kumbukirani kuti dziko la Yemen ndilogawikana moti mzinda waukulu wa dziko-lo (capital city Sanaa) uli m'manja mwa asilikali othandizidwa ndi Iran otchedwa ma Houthis ku Yemen komanso mizinda ina maka ya m'mphepete mwa nyanja koma Bab al Mandeb Strait yeniyeni yo inali mmanja mwa asilikali a boma omwe akulamulira mbali ina ya dziko-lo koma ndi ofooka moti Ma Houthis amavutika nawo kwambiri kubandulidwa.

Boma la Yemen limathandizidwa ndi Saudi Arabia komanso kuthandizidwa ndi maiko osianasiana kuphatikizapo America ndi Europe pomwe Iran imathandiza ma Houthis. Dera lomwe ma alandalo ndilofunika kwambiri ndipo asilikali a boma a dziko la Yemen athawa kale mu dera-lo.

10/09/2026

BREAKING NEWS: Ndege 9 za dziko la America zomwe zinali mu kampu ya asilikali a America ku Jordan zaphulitsidwa. ๐Ÿ‘‰Aljazeera

America yaphulitsa sitima zisanu za Iran zomwe zimanyamula mafuta (oil tankers) mu Strait of Hormuz. Iran ndiyomwe inaya...
09/09/2026

America yaphulitsa sitima zisanu za Iran zomwe zimanyamula mafuta (oil tankers) mu Strait of Hormuz. Iran ndiyomwe inayambitsa kuphulitsa sitima zankhondo ziwiri za dziko la America zomwe akuzigwiritsa ntchito panyanja zija (aircraft carrier & navy destroyers) moti mpakana zinathawira ku malo ena koma mu nyanja yomweyi.

Zitatero America nayo inaphulitsa zina mwa sitima zomwe Iran imazigwiritsa ntchito popititsa mafuta ku msika. Lero Iran inavunganso mabomba ena kuphulitsa sitima zankhondo ziwiri za dziko la America ndipo zitatero America nayo siyinachitire mwina koma kuphulitsa sitima zisanu zomwe zimanyamula mafuta za dziko la Iran __ akuyendera nyo kwa nyo anthuwa, vunga nane ndivungeko. Cholinga cha Iran ndikuthamangitsa sitima zankhondo za dziko la America mu nyanja ija ya Gulf of Oman kapena mu Persian Gulf komwe akumaimitsa sitima zawo za nkhondo ndikumaphulitsa zinthu ku Iran.

America ikudziwa bwino kuti ngati Iran ingapitirize zoterezi apo ndiye kuti mphamvu ya America olo zomatchingira sitima za malonda zija zitha kuchepa ndipake nawo akuphulitsa sitima za Iran kuti mwina asiye zawozo.

Tili pankhani ngati yomweyi nayo Saud Arabia ikulira kuseliku asilikali otchedwa ma Houthis ku Yemen ataphulitsa zitsime zikuluzikulu zamafuta zomwe dziko-lo limadalira kwambiri koma akuti abwezera ngakhare kuti ndi Saudi Arabia yomweyo ndi yomwe inayambitsa pophulitsa ma Houthis . Izi zikuchitika pamene
nkhondo ya pa chiweniweni ikupitilirabe ku Yemen pakati pa Houthis komanso asilikali a boma a dzikola Yemen.

Omvera kumbukirani kuti dziko la Yemen linagawikana pawiri pamene ma Houthis analanda mzinda waukulu wa dziko-lo otchedwa Sanaa mu chaka cha 2014 ndi madera ena komwe ma Houthis akulamulira.

Breaking News:  Iran yalanda ngalawa kapena kuti boti la nkhondo la dziko la America mu nyanja ya Strait of Hormuz. Boti...
08/09/2026

Breaking News: Iran yalanda ngalawa kapena kuti boti la nkhondo la dziko la America mu nyanja ya Strait of Hormuz. Boti laling'ono limeneri ndi lija limatchedwa unmanned Submersible kapena kuti boti loyenda pansi pa madzi koma losakweramo anthu. Boti ili lagwidwa pamene limalowa mu Strait of Hormuz.

07/09/2026

Amaikonda "The Nyasaland Post" ndi angati aimike manja tiwone? ๐Ÿ™‹โ€โ™‚๏ธ๐Ÿคš Tili ndi zambiri pamudzi pano zikubwera ndithu. ๐Ÿ˜

Dziko la Ukraine lapempha dziko la Russia kuti nkhondo iyime kaye kumbali zonse monga kuphulitsana ndikumenyana komwe ku...
05/09/2026

Dziko la Ukraine lapempha dziko la Russia kuti nkhondo iyime kaye kumbali zonse monga kuphulitsana ndikumenyana komwe kuli mkati pakati pa asilikali a maiko awiri-wa kuti pachitike zokambirana zothetsa nkhondo.

Komabe Ukraine yati Russia siyinayankhebe pa pempholi ndi pamene leronso aiphulitsa Ukraine ndikuphako anthu asanu posachedwapa. Akuluakulu a dziko la America Steve Witkoff komanso Jared Kushner tikunena pano ali mu mzinda wa Moscow ku Russia komwe akukambirana zokhudza kuthetsa nkhondo imeneyi ndipo anthu omwewa apitanso ku Ukraine akachoka ku Russia ko.

TO WHOM IT MAY CONCERN: The battle for future presidency  is underway, everyone will fight hard to sell themselves to th...
04/09/2026

TO WHOM IT MAY CONCERN: The battle for future presidency is underway, everyone will fight hard to sell themselves to the citizens but it's doubtful whether nationals will buy it so soon. After fighting a common enemy 11 months ago, they've now opted to launch another senseless war from within and we have seen it for a while.

That poor country has always been like that under every regime __fighting one another for no reasons instead of concentrating on development activities and economic growth. After their nonsensical arguments, it's eventually citizens who pay the price. What that man said is non but the truth and of course the truth that was supposed to ensure respect for their government and the leader. There are always problems in every regime but criticising each other in public instead of consulting each other first is not only silly but a complete madness aimed at seeking attention and imposing oneself as wise and better to the citizens for personal benefits.

A foolish wife chooses to solve her family problems by announcing her differences with the husband to neighbors or friends instead of discussing the matter and solving them internally. Too much cooks spoils the broath. Citizens won't benefit from fighting, it will only expose stupidity and weaknesses giving chance to opposition to shine.
___The Nyasaland Post

Address

Limbe
Blantyre
4052

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when The Nyasaland Post posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to The Nyasaland Post:

Shortcuts

Share