26/06/2025
MADEMO LERO AWONESA ZOTI MDZIKO MUNO KUTSOGOLOKU MUBUKA NKHONDO
Zomwe zachitika mu mzinda wa Lilongwe pamene apolisi komanso asilikali ankhondo amayang'anira anthu onyamula zikwanje a MCP akumenya mkulu amene amatsogolera ziwonetsero, Sylvester Namiwa komanso kusokoneza ziwonetserozi, zikutsutsana ndi zomwe akuluakulu a nthambi za chitetezo m'dziko muno analonjeza m'mbuyomu.
A Maxwell Mwachande omwe amayendetsa minibus mu mzinda wa Lilongwe ndipo anthu ena osadziwika bwino atentha minibus yawo yomwe anayimika pa community ground kumapanga zabizinesi yawo.
Malinga ndi kulankhula kwa a Mwachande anthu osadziwika bwino atentha minibusiyi kamba koti mtsogoleri wa zionetsero a Sylvester Namiwa anathawira mu basiyi anthu ena osadziwika bwino akufuna kuwakhapa ndi zikwanje.
Galimoto inanso ya 2 Toner yaotchedwa ndi anyamata azikwanjewa kumalo azionesereku omwe anatuluka kumaloku pa galimoto ya Toyota Fortuner.
Lolemba sabata lino, bungwe la MEC lidakumana ndi akuluakuluwa ku Mangochi komwe adalonjeza kuti awonetsetsa kuti aliyense ndi otetezedwa pamene dziko lino likukonzekera chisankho cha pa 16 September 2025.
Mkulu wa polisi, Merlyne Yolamu adati nthambi yake komanso ndi nthambi zina ndi zokonzeka kupereka chitetezo kwa aliyense mosakondera komanso mosasankha mbali.
"Tidali pa mkumano ndi nthambi zina zimene zimapereka chitetezo a MDF, Prison, Immigration komanso ayini akefe apolisi amene udindo wathu ndikupereka chitetezo cha mdziko. Tiri patsogolo pokhwimitsa chitetezo munyengo ino ya chisankho," iye adatero.
Izitu zadandawulitsa anthu mdziko muno ndipo ena mwa iwo, awonetsa kukhumudwa ndi kukula kwa mchitidwe wa anthu onyamula zikwanje, kwambiri ku Lilongwe, omwe akumalepheretsa kuchita ziwonetsero mumzindau.
A Namiwa amenyedwa koopsa pa maso pa asilikali ndi apolisi ndipo a Ayesa kupempha thandizo kuchokera kwa achitetezowa koma iwo amangoonerera Namiwa akumenyedwa ndi anyamata a MCP ati kamba kochita zionesero zokwana wamkulu wa mec Mayi Anabel John Tembo Mtalimanja.
Pa chisankho ichi ziko lisokonekera ili.
Padakali pano Dr Dalitso kabambe anapangitsa press briefing yodzudzula mchitidwe omwe wachitika ku ma demonstration ku Lilongwe,komwe nkulu otsogolera ziwonetselozo a Silvester Namiwa amenyedwa modetsa nkhawa ndi zigawenga za MCP pomwe a Police ndi asilikali (MDF) akuwonelera koma osachitapo kanthu.