24/11/2025
M'nyamata wazaka 19 Madalitso Chitani wam'mudzi Tchatatcha m'dera la mfumu yaikulu Mlolo m'boma la Nsanje wadzipha atasemphana maganizo ndi bambo ake.
Wachiwiri kwa m'neneli wa apolisi m'boma la Nsanje Jabulani Ng'oma wati lamulungu bambo wa m'nyamatayu Winfold Chitani anasowa lamya yake yam'manja ndipo amakaikira kuti iye ndiye wasowetsa lamyayo.
Ng'oma wati kutsatira kusamvana komwe kunalipo pakati pa awiriwa, m'nyamatayu mwachinunu anachoka ndikukalowa mugowelo lake komwe anatenga chingwe ndikuzikhweza kudenga lanyumba.
Apolisi ochokera ku Fatima omwe anatsagana ndi madotolo ochokera kuchipatala cha mission cha Trinity atachita kauniuni pathupi la m'nyamatayu, zotsatira zake zasonyeza kuti wafa kaamba kobanika.
Wolemba: Manford Chirombo