04/05/2026
OSEWERA AKUKANIKA KUGOLETSA ZIGOLI watero Chirwa
Mphunzitsi wa FCB Nyasa Big Bullets, Gilbert Chirwa, wati osewera ake pena akulephera kugwiritsa bwino mpata omwetsa zigoli kamba koti sanagwirane.
Chirwa walankhula izi dzulo timuyi itagonjetsa Mafco 1-0 chigoli chomwe Vitumbiko Phiri anadzigoletsera yekha mu 2026 FDH Bank Premiership pa bwalo la Joyce Chitsulo m'boma la Mwanza.
Chirwa wati ayesetsa kukonza mavutowa kuti akamakumana ndi Mighty Wanderers kumathero a sabatayi chili chonse chikhale chili m'chimake.
Bullets tsopano ili panambala yachinayi ndimapointi anayi pamasewero awiri omwe asewera.