11/05/2026
Bwalo la Kalichero Magistrate m'boma la Ntcheu lalamula a Chifundo Samson kuti asapalamulenso kwa miyezi 36, apo biii! akakhala kundende miyezi makumi awiri (20) ngati angapalamule.
Oyimira boma anauza bwaloli kuti a Samson anaba zitsulo zopangira mawindo, koma zinapezeka pano zili m'manja mwamwini wake, komanso mkuluyu amkafuna kudzipha yekha momwe anali kodikilira mulandu kundende ya Ntcheu.
Oweruza mlandu Magistrate Pleasant Sichari, walamula a Samson kuti akhale mfulu koma asapalamurenso kwa miyezi 36.
"Kaya mkazi wanu akakuputani, kapena wina kukuyambani, kukumenyani, kawapeweni onsewo powauza zoti chilango muli nacho kale mkhosi mwanu," anatero Magistrate Sichari pomaliza ndi chigamulo chake.
Wolemba: Hudson Nkumbira, Ntcheu