Nation Publications Limited

Nation Publications Limited Established in 1993, Nation Publications Ltd is an award-winning media house providing credible news

Nation Publications Limited, Publishers of The Nation, Weekend Nation, Nation On Sunday, Nation Online and Fuko

16/09/2025



Pamene nthawi imakwana 6:25 pa malo ovotera a Namatete ku Blantyre City Constituency anthu anali asanayambe kuponya voti.

Akuluakulu a Mec ali pakalapakala kulongosola zina ndi zina komanso kukambirana ndi anthu oimira zipani.

Anthu ena ayamba kudandaula kaamba kakuchedwaku.

Malingana ndi bungwe la Mec, kuvota kutsekedwa 4 koloko madzulo ano.

(Wolemba Mathews Kasanda)

  As the sun rose over Kabwazi School Polling Centre in Ntcheu Central East, queues of eager voters grew steadily.One of...
16/09/2025




As the sun rose over Kabwazi School Polling Centre in Ntcheu Central East, queues of eager voters grew steadily.

One of them, 58-year-old Gelliat Mbewe, said voting made him break his daily routine. He usually waters his cabbage and tomato garden at 3 a.m., his main source of livelihood.

“But today is different. Farming can wait. After all, we farm every day—voting comes once every five years. That’s why today is special. I need to do this. Chikwanje changa ndatenga kale (I have my weapon handy),” he said.

The polling centre has 812 registered voters expected to cast their ballots today.

(Report by Fatsani Gunya-Correspondent)

16/09/2025




Pomwe 6 koloko yakwana ndipo dongosolo loti anthu ayambe kuvota pa malo a Njedza m'dera la Mulanje South lili mkati, anthu akuona kuchedwa kuti aponye voti ndipo akumemeza oyendetsa chisankho kuti achite machawi. Iwo ati atopa.

(Wojambula ndi kulemba: Temwa Mhone)

    Nthawi m'mene imakwana 4 koloko m'mawa uno anthu anali atayamba kale kubwera pa Mwanazanga Primary school yomwe ndi ...
16/09/2025




Nthawi m'mene imakwana 4 koloko m'mawa uno anthu anali atayamba kale kubwera pa Mwanazanga Primary school yomwe ndi imodzi mwa malo oponyera voti mu dera la Machemba ku Phalombe.

A Lapken Langwani, m'modzi mwa ovota komanso omwe anali oyambilira kufika, ati anachiona chanzeru kuti abwere chifukwa voti ndiyomwe imasankha anthu omwe ukufuna ngati atsogoleri.

(Wolemba: Maggie Tembo-Correspondent )

    Apa ndi pa Rumphi Magistrate's Court, malo oponyera voti pa chisankho cha lero. Anthu Ayamba kufika m'ma 4:45am kuti...
16/09/2025




Apa ndi pa Rumphi Magistrate's Court, malo oponyera voti pa chisankho cha lero. Anthu Ayamba kufika m'ma 4:45am kuti adzaponye voti yawo.

(Wolemba: Taonga Chizinga Nyirenda-Correspondent)

16/09/2025



Pamene imakwana 5:15 am nkuti gulu la anthu litayamba kusonkhana pamalo oponyera voti la St. Michael F.P school m'boma la Chiradzulu.

Anthu okwana 3049 ndi omwe akuyenera kuponya voti ya mtsogoleri wadziko, phungu wanyumba yamalamulo komanso khansala pa sukuluyi.

Kanema ali munsiyu akuonetsa omwe akuyendetsa chisankho pa malowa akuchita zokonzekera.

📹Wisdom Chirombo

(Wolemba Wisdom Chirombo-Correspondent)

  Apa ndi pa Sukulu ya Sekondale ya Liwonde m'boma la Machinga, pomwe anthu lero akuyembekezera kuponya voti yosankha mt...
16/09/2025




Apa ndi pa Sukulu ya Sekondale ya Liwonde m'boma la Machinga, pomwe anthu lero akuyembekezera kuponya voti yosankha mtsogoleri wa dziko, Phungu komanso Khansala.

Ena mwa anthu omwe tacheza nawo pa malowa, monga a James Nkhongoza, ati adzuka 4 koloko m'mawa uno ulendo wokaponya voti pofuna kukwaniritsa ufulu wawo wosankha adindo omwe iwo akuwafuna.

Ndipo a Peter Nyoni alimbikitsa anthu kutuluka mwaunyinji ndi kukaponya voti ponena kuti iwo akudziwa bwino za kuipa kosatenga nawo gawo pa chisankho.

(Wolemba: Haneeph Maulana -correspondent)

16/09/2025




Pemene nthawi imati 5:15 m'mawa uno gulu la anthu linali litayamba kale kusonkhana pa malo oponyera voti a St. Michael F.P school m'boma la Chiradzulu.

Anthu okwana 3049 ndi omwe akuyenera kuponya voti ya mtsogoleri wa dziko, phungu wanyumba ya malamulo komanso khansala pa malowa.

Kanema ali m'munsiyu akuwonetsa omwe akuyendesa chisankho pa malowa akuchita zokonzekera:

(Wolemba ndikujambula: Wisdom Chirombo-Correspondent)

   Mmene imakwana 5:10am anthu ochuluka anali atafika kale pa malo oponyera voti a Thyolo Prison omwe akupezeka mu wodi ...
16/09/2025



Mmene imakwana 5:10am anthu ochuluka anali atafika kale pa malo oponyera voti a Thyolo Prison omwe akupezeka mu wodi ya Mchima mu dera la Thyolo Central.

(Wolemba: Ted Likombola - Correspondent)

16/09/2025



As time struck 4:45am, setting up of equipment has started at Nayizi Primary School ground, one of the polling centres in Blantyre City Chigumula, BCA, Club Banana Constituency.

Polling staff and monitors of various parties are als arriving.

(Repory by Michael Mmeya)

   Arriving at Nayizi Primary School, one of the polling centres in Blantyre City Chigumula BCA - Club Banana Constituen...
16/09/2025



Arriving at Nayizi Primary School, one of the polling centres in Blantyre City Chigumula BCA - Club Banana Constituency at 3.30am, l find a man and a woman already there, and l hear them making calls to friends and relatives to come out and vote early and go to do other things. The two say they were here at 3 am. In three minutes we are joined by two women.

"Tivote tipume abale inu (let us vote and rest)," says one of the women.
And they are heard asking each other if they have not forgotten what they are referring to as "Chikwanje", meaning their voter registration card.

Blantyre City Chigumula BCA - Club Banana Constituency has three wards, namely; Chigumula Club Banana, BCA Hills Chigumula and Bangwe Namiyango.

The three wards have 19 local government aspirants, including seven independents and representatives of all other parties
Consipicuosly missing in the ward councillors' race are Aford and Peoples Party.

Those fighting for the Parliamentary seat in this constituency are Golden Lungu for MCP, Peter Mvalo (UDF), Wild Ndipo (Independent) and Sameer Suleman (DPP).

(Report by Michael Mmeya)

15/09/2025




Pamene Amalawi akhale akuponya voti, tamwaza atolankhani athu ponseponse amene azikupatsirani momwe chisankhochi chikuyendera. Sitikugona ngati ambirinu.

Izi zili apo, chonde kumbukirani izi:

Osavala makaka a chipani kapena shado amene mukumufuna popita kovota.

Mukavota, osamangoti yaviyavi pa malo ovotera.

Osajambula chithunzi cha momwe mwavotera ndi kutumiza m’masamba a mchezo.

Musaulule mmene mwavotera kwa ena kufikira mtunda wa mamita 100 kuchojera pa malo ovotera.

Pasakhale zinthu za kampeni mamita 200 kuchokera pa malo ovotera.

Kwa okonda chakumwa cha tsooo, ndi pempho lathu kuti mukonkhe kummero mutavota kuopa kusankha molakwika.

Address

Salmin Amour Road
Chichiri

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Nation Publications Limited posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Nation Publications Limited:

Share