03/09/2025
Akatswiri omwe amalankhula pa nkhani zosiyana siyana ati ndi zokhumudwitsa kuti ufulu wa olembankhani ukupitilira kuphwanyidwa dziko muno.
Iwo alankhula izi pomwe mmodzi mwa olembankhani a wailesi ya Chibvomelezi David Nota analetsedwa kugwira ntchito yake pa malo pomwe mmodzi mwa omwe akupikisana nawo pa mpando wa phungu wa ku nyumba ya Malamulo mdera la kummwera kwa boma la Chikwawa, Luckson Ngalu amachitsa msonkhano wawo okopa anthu kudzawasankha pa chisankho chomwe chichitike pa 16 mwezi uno.
Izi zachitika pa malo ochitira malonda a Nsangwe mboma la Chikwawa.
Koma pomwe olemba nkhani wathuyu amagwira ntchito yake pa malo a msonkhanowu, anthu otsatira Ngalu anayamba kumugwiragwira, kenako kumulanda zida zake zogwilira ntchito.
Pochita izi, otsatirawa amamunena olembankhaniyu kuti watumidwa pa malowa ndi anthu ena omwe akupikisana ndi a Ngalu kudelali.
Ndipo pomwe zimachitika izi, ma kanema komanso zinthuzi zomwe iye anali atajambula pa malowa ati zosonyeza a Ngalu akugawa ndalama kwa anthu ndi zina, zinafufutidwa ndi anthuwa.
Koma a Ngalu omwe pa nthawiyo anali pamalo a ziwawawo uku akuwonelera izi zikuchitika, sakuyakha lamya zanthu za manja kwa nthawi zingapo zomwe takhala tikuwayimbira pa nkhaniyi.
Ndipo polankhulapo pa nkhaniyi, bungwe lophunzitsa zinthu zosiyanasiyana la NICE, lati zomwe zachitikazi ndi zodandaulitsa komanso zosemphana ndi malamulo a utolankhani mdziko muno.
Malingana ndi mkulu wa bungweli m’boma la Chikwawa, Chiyembekezo Gwazayani, kuletsa atolankhani kapena munthu wina kucheza ndi anthu omwe ali pa misonkhano yokopa anthu kapena kuwaletsa kujambula zithunzi, ndi mlandu kutengera ndi ndime 33 ya lamulo la Political Parties la chaka cha 2018.
Gwazayani wati munthu akapezeka akuchita izi monga momwe a luckson Ngalu achitira ndi anthu awo owatsatira, amapeleka chindapusa chandalama.
Naye Katswiri olakhulilapo pa nkhani zosiyanasiyana mdziko muno Humphreys Mvula wati ndi zokhumudwitsa kuti ufulu wa atolankhani ukupitilira kuphwanyidwa dziko muno.
Mvula wati izi ndi zosephana ndi malamulo a utolankhani maka mu nyengo ino yokopa anthu kudzatenga mbali pa chisankho chikudza.
Chomcho Mvula walangiza atsogoleri a ndale kuti asiye kuchita izi ponena kuti atha kuchotsedwa pa ndandanda wa anthu omwe akupikisana nawo pa zisankho zomwe zilipo mwezi uno akadzapezeka olakwa ngati mabungwe ena omenyera ufulu wa atolankhani mdziko muno angapitilire kuyikoka nkhaniyi.