17/11/2025
Mtsogoleri wa kale wa dziko lino Lazarus Chakwera wanenetsa kuti achilimika potsogolera chipani cha Malawi Congress (MCP) kuti chipanichi chidzabwelerenso m'boma m'chaka cha 2030.
Chakwera wayankhula izi lero mu mzinda wa Lilongwe pa msonkhano wa atolankhani pomwe wapemphanso otsatira chipanichi kuti akhale ogwirizana ndi osunga bata kuti zimenezi zidzatheke.
Pa msonkhanowu iye wauza atolankhani kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wavomera kuti iye angathe kupita m'dziko la Tanzania kuti akakhale nawo pa zokambirana zothandiza kudzetsa bata ndi mtendere m'dzikolo potsatira ziwawa zomwe zinachitika m'dzikolo mutachitika chisankho.