
18/07/2025
KUTHETSEDWA KWA BUNGWE LOYENDETSA ZITSANKHO M'DZIKO LA BURKINA FASO
Akuluakulu ankhondo m'dziko la Burkina Faso pansi pa ulamuliro wa Ibrahim Traole athetsa bungwe lowona za zisankho m'dzikolo ponena kuti limaononga ndalama.
Zateremu, unduna owona za m'dziko ndi omwe uzidzayendetsa zisankho mtsogolomu.
Nyumba yosindikiza nkhani ya AFP yagwira mawu a nduna ina, Emile Zerbo yomwe inafotokoza kuti bungwe loyendetsa zisankho limathandizidwa ndi ndalama zokwana $870,000 zomwe ndi pafupifupi K1,503,541,830, ndalama yakuno ku Malawi pa chaka.
Zerbo wati kuthetsa kwa bungweli kulimbikitsa ulamuliro odzilamulira komanso kuchepetsa zisonkhezero zakunja.
Mizwanya Fm Community Radio
Source: BBC