
23/11/2021
INENSO NIDZAKUKANANI
Mchaka cha 1994 mudzi wina m'boma la mchinji T/A Mduwa mudachitika nkhani yachilendo komanso yochititsa tsemwe.
Bambo wina wachuma,Odziwika bwino komanso waulemu wake adagonana ndi mtsikana wa misala indeee wozerezeka baba, Patsikuli mkazi wake adachokapo ndipo iye adapezerapo mwayi omuyitanira kuchipinda ndipo adamugwira pakamwa kuti asakuwe pamapeto pake adamupatsa ndalama ndizinthu zina zambiri.Tsikuli potengera kuti banjali limakhala lotangwanika ndi mabizinesi awo mkuluyu adapezerapo mwayi okongodzeratu mphanvu zake zonse mbali inayi wamsalayu amangoti kukhala sikoma tereeee.
Poti mimba mchulu ntchembere zidadabwa maonekedwe ake ndipo zidakonza zomufunsa, Kodi Chaku ukuoneka kuti uli nimimba zili bwanji apa iyeyu amangoseka osayankhapo Kathy poti mimbayo samayidziwa olo pang'ono, Mayi wina adamufunsapo ngati adagonanapo ndi wina aliyense kwinaku akuyeserera muja zikhaliramu apapa mpamene Namwaliyu adasokhanitsa nzeru ndipo adayamba kusekerera pokumbukira mmene Bambo uja amachera chambo ndipo adafotokoza zonse mmene zidamuchitikira patsikulo.
Pabwalo pa aMfumu mponda matiki uja adalalata kwambiri kuti iyeyo mkazi alinaye komanso wamaonekedwe sangataye nthawi kugonana ndi munthu wamisala, osasamba komanso buthu ngati ili aaii.
Amfumu amudzi adadandaura pakuti Chaku adalibe makolo onse awiri adamwalira kale kale.
Patapita miyezi ingapo Namwali uja adabadwitsa mwana wa mamuna ndipo madokotala ndi adafotokozera nkhaniyake yonse kwa mzungu ndipo zidamukhudza ndipo iye adatenga Chaku pamodzi nikhandala ulendo wakwawo patatha zaka zochuluka mwana wa Chakumanda adabwera kumudzi kwawo kukakhala ali Olemera komanso Ophunzira zedi.
Bambo aja adali atasauka kwambiri akazi awo adafa ndipo adapita kukapemba kwa Mwanayo ndipo adati pepa mwana wanga ndidachita molakwa nidakukanani koma khululukire Mwana wanga sininkadziwa , Ndipo Mwanayo adati Yesu christu adanena kuti nonsenu;ONIKANA INE, INENSO NIDZAMKANA PAMASO PA ATATE ANGA akumwamba.
AMEN