30/05/2026
Timu ya Luanar Mitundu lero (loweruka) yadzidzimutsa ndi kubatiza timu ya Civil Service United ndi zigoli zitatu kwa duu pa bwalo la masewero la Dedza, mu mpikisano wa FDH Bank Premiership.
Katswiri wa timu ya Mitundu Moses Nyirenda anali oyamba kuboola ukonde patadutsa mphindi 41 m'chigawo choyamba, asanabwele Raheem Mtondera m'chigawo chachiwiri ndi zigoli zake ziwiri, kusiya ochemelela timu ya Civo omwe zinthu sizikuyendabe, ali zolizoli.
Nayo timu ya Ekhaya FC, kukumana koyamba ndi timu ya Masters FC, yadya bwino ndi zigoli ziwiri kwa duu pa bwalo la masewero la Mpira mu mzinda wa Blantyre.
Tmu ya Blue Eagles ikupitilira kuchita modabwitsa pomwe yagonjetsa timu ya Creck Sporting Club ndi zigoli ziwiri kwa duu pa bwalo la Dimba ku Mchinji.
Ku Lilongwe timu ya Silver Strikers yagonjetsa timu ya Mafco FC ndi chigoli chimodzi kwa duu pa bwalo la Silver, kudzera mwa Ernest Petro kuti ibwele pa mwamba pandandanda wa matimu 16.
Daniel Philimon, Salima
Linga FM Online