Linga FM Online

  • Home
  • Linga FM Online

Linga FM Online Welcome to the official page for Linga FM Radio, follow for more & important updates.
(1)

   Timu ya Luanar Mitundu lero (loweruka) yadzidzimutsa ndi kubatiza timu ya Civil Service United ndi zigoli zitatu kwa ...
30/05/2026




Timu ya Luanar Mitundu lero (loweruka) yadzidzimutsa ndi kubatiza timu ya Civil Service United ndi zigoli zitatu kwa duu pa bwalo la masewero la Dedza, mu mpikisano wa FDH Bank Premiership.

Katswiri wa timu ya Mitundu Moses Nyirenda anali oyamba kuboola ukonde patadutsa mphindi 41 m'chigawo choyamba, asanabwele Raheem Mtondera m'chigawo chachiwiri ndi zigoli zake ziwiri, kusiya ochemelela timu ya Civo omwe zinthu sizikuyendabe, ali zolizoli.

Nayo timu ya Ekhaya FC, kukumana koyamba ndi timu ya Masters FC, yadya bwino ndi zigoli ziwiri kwa duu pa bwalo la masewero la Mpira mu mzinda wa Blantyre.

Tmu ya Blue Eagles ikupitilira kuchita modabwitsa pomwe yagonjetsa timu ya Creck Sporting Club ndi zigoli ziwiri kwa duu pa bwalo la Dimba ku Mchinji.

Ku Lilongwe timu ya Silver Strikers yagonjetsa timu ya Mafco FC ndi chigoli chimodzi kwa duu pa bwalo la Silver, kudzera mwa Ernest Petro kuti ibwele pa mwamba pandandanda wa matimu 16.

Daniel Philimon, Salima

Linga FM Online

Anthu  mu mzinda wa Mzuzu okonda ndi kutsatira timu ya mpira wa miyendo ya ku Mangalande ya Arsenal, ayamba ulendo wa nd...
30/05/2026

Anthu mu mzinda wa Mzuzu okonda ndi kutsatira timu ya mpira wa miyendo ya ku Mangalande ya Arsenal, ayamba ulendo wa ndawala kukondwelera kupambana kwa timu yawo pa mpikisano wa English Premier League (EPL), pomwe Arsenal yakhala akatswiri a ligiyi patadutsa zaka 22.

Ngati mbali imodzi ya chikondwererochi, ochemelerawa akuyembekezekanso kupereka zipangizo zothandizira ntchito za ukhondo mu mzindawu ku khonsolo ya Mzuzu.

Arsenal yapambana chikho cha EPL koyamba kuchokera mchaka cha 2004, zomwe zadzetsa chisangalalo pakati pa anthu okonda timuyi padziko lonse la pansi kuphatikizapo a mu mzinda wa Mzuzu.

Wolemba Chisomo Lapken, Mzuzu
Linga FM Online

30/05/2026

A Gerald Banda a zaka 32 omwe ndi m'phunzitsi wa pulayimale ali m'manja mwa apolisi m'boma la Kasungu kamba kowaganizila kuti amagonana ndi msugwana wa wa sukulu wa zaka 16.

Malingana ndi wachiwiri kwa m'neneli wa polisi ya Kasungu Sergeant Miracle Hauli, a Banda akhala ali pa ubwezi ndi msungwanayu kuchokela chaka chatha msugwanayu ali mu sitandade 7 ndipo izi zakhala zikulowetsa pansi kukhoza kwake m'kalasi.

Msungwanayu adawulula za ubweziwu kwa makolo ake koma sadachitepo kanthu, ndipo adaganiza zouza m'phunzitsi wamkazi pa sukulupo yemwe adamulangiza kukanena nkhaniyi ku polisi ya Chisinga ndipo atalandila dandauloli apolisi adathamanga kukamanga a Banda.

A Banda amachokela m'mudzi wa Nkhuzenje m'fumu yaikulu Simulemba m'boma la Kasungu ndipo akawonekela ku bwalo la milandu posachedwapa.

Wolemba Raphael Mapira Kasungu.

Linga FM Online

.

MUTHARIKA AGAWA UNDUNAYemwe anali wachiwiri kwa nduna ya ulimi ndi chitukuko cha madzi a Thoko Tembo, omwenso ndi phungu...
29/05/2026

MUTHARIKA AGAWA UNDUNA

Yemwe anali wachiwiri kwa nduna ya ulimi ndi chitukuko cha madzi a Thoko Tembo, omwenso ndi phungu wa nyumba ya malamulo wadela la kumpoto kwa boma la Neno, amusankha kukhala nduna ya migodi.

Mlembi wa boma a Justin Saidi alengeza izi mkalata usiku uno, ponena kuti mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika agawa unduna wa mphamvu za magetsi ndi mafuta ndi migodi.

Izi zikutanthauza kuti Dr. Jean Mathanga tsopano ndi nduna yowona mphamvu za magetsi ndi mafuta basi. A Saidi ati a Mutharika asintha ndunazi pogwiritsa ntchito mphamvu za malamulo a dziko lino.

Pakadali pano, bungwe la lomenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati zikanakhala bwino kuchepetsa chiwerengero cha nduna kulekana ndi kuwonjezera pofuna kupulumutsa chuma cha boma.



 Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yachotsa ntchito yemwe amagwilizira udindo wa mphunzitsi wa timuyi a Gilbert Chirwa.A Chi...
28/05/2026



Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yachotsa ntchito yemwe amagwilizira udindo wa mphunzitsi wa timuyi a Gilbert Chirwa.

A Chirwa anatenga ntchitoyi mwezi wa December timuyi itachotsa ntchito yemwe anali mphunzitsi wamkulu a Peter Mponda.

Timuyi sabata yatha yachititsa mayeso anthu asanu omwe analembera kufuna ntchito ya u phunzitsi wa timuyi.

Ena mwa omwe achita nawo mayeso ofuna ntchito ndi monga a Mark Harrison, Etson Kadenge, komanso a Gerald Phiri Senior.

Daniel Philimon, Salima

Linga FM Online

The introduction of the National Mathematics Carriculum Reform Program is said to have contributed to the high enrolment...
27/05/2026

The introduction of the National Mathematics Carriculum Reform Program is said to have contributed to the high enrolment of pupils which is creating demand for more classrooms and qualified teachers across Malawi.

UK All-Party Parliamentary Group on Global Education Chairperson Bambos Charalambous says the challenges observed need more support to be resolved and assured local authorities that he will encourage the UK government to prioritize education sector in the country.

This has been disclosed today (Wednesday) during a UK Parliamentary delegation on Education visit to Thundu and Kaphatenga Primary Schools in Salima to appreciate progress of the program.

Meanwhile, National Mathematics Curriculum Reform National Coordinator Sakayi Musopole says the initiative has transformed the country's education system into one that is practical, inclusive and focused on skills development and bridged numeracy skills' gap among the learners.

By Daniel Philimon, Salima



Zikhulupiliro za chipembedzo ndi za chikhalidwe akuti ndi zina mwa zinthu zomwe zikukolezela m'chitidwe okana kulandila ...
27/05/2026

Zikhulupiliro za chipembedzo ndi za chikhalidwe akuti ndi zina mwa zinthu zomwe zikukolezela m'chitidwe okana kulandila akatemela osiyanasiyana m'boma la Kasungu.

Mkulu owona za umoyo ndi ukhondo m'bomali a Emmanuel Golombe anena izi pa mkumano omwe akuluakulu achipatala cha Kasungu anali nawo ndi atolankhani wofuna kulimbikitsa mgwilizano wa ntchito pakati pa nthambi yoona za umoyo ndi atolankhani m'bomali.

Pamene akukonzekela kupeleka katemela wachitatu wa Polio m'bomali kuyambila lachiwiri pa 2 June kufikila pa 5 June, a Golombe ati makolo akuyenela awonetsetse kuti ana awo alandilanso katemelayu kachitatu kuti agwile bwino ntchito yoteteza anawa ku nthenda ya polio.

Ndipo wapampando wa bungwe la abusa m'bomali a Justin Zika Banda wachenjeza atsogoleri azipembedzo za mchitidwe oletsa owatsatila kulandila katemela ponena kuti kutelo kumayika miyoyo ya ana pa chiopsezo.

Wolemba Raphael Mapira Kasungu

Linga FM Online

Boma lati a Malawi asakhale ndi nkhawa kuti ndalama za mthumba la chitukuko la CDF zisakazika chifukwa lakhadzikitsa ndo...
27/05/2026

Boma lati a Malawi asakhale ndi nkhawa kuti ndalama za mthumba la chitukuko la CDF zisakazika chifukwa lakhadzikitsa ndondomeko zosamalira chumachi kuti chipindulire a Malawi okhala m'madela aku mudzi.

Nduna ya maboma aang'ono ndi chitukuko a Ben Phiri anena izi kwa atolankhani m'mawa uno mu mzinda wa Lilongwe pofuna kupereka tsatane-tsatane wa momwe makhonsolo akonzekera kugwira ntchito za chitukuko zomwe anthu akufuna.

Iwo ati alembanso anthu oyenera kugwira ntchito m'makhonsolo onse a m'dziko lino ndi cholinga chakuti ntchito zomanga-manga zikhale zaukadaulo komanso zolimba.

Boma lipereka ndalama zokwana K5 billion m'dela lililonse la phungu pa chaka.



25/05/2026

Anthu okwiya pa sitolo za Kawamba m'boma la Kasungu apha bambo yemwe akumuganizila kuti anaba njinga mtawuni ya Kasungu.

Wachiwiri kwa m'neneli wa apolisi m'bomali Sergeant Miracle Hauli wati munthu yemwe amuphayu pamodzi ndi mzake yemwe wathawa, anakwela njinga yamoto ya a Duncan Zimba kuchoka mu tawuni ya Kasungu kupita m'dela la Kayesa.

Atafika malo ena, awiriwa anawathila tsabola m'maso a Zimba nkuwakankhila pansi ndi kuthawa ndi njingayo kulowela kwa Kawamba. Koma a Zimba anadziwitsa akabaza anzawo akwa Kawamba omwe anakwanitsa kulanda njingayi ndikugwila m'modzi mwa awiriwa ndikuyamba kumumenya. koma achitetezo a m'mudzi anakwanitsa kulanditsa malemuwa ndikumutsekela mu m'chitokosi cha pa bwalo la milandu la Kawamba.

Anthu okwiyawa anamemana ndikuthyola chitokosicho ndikumenya malemu wo mpaka kupha. Pakadali pano apolisi akusakasaka omwe achita izi komaso woganizilidwa kuba njinga yamoto yemwe wathawayo.

Wolemba Raphael Mapira Kasungu



25/05/2026

Mayi yemwe sakudziwika akuti wataya khanda lomwe achipatala akuliganizila kuti ndi lochepela masiku anayi m'dela la m'fumu yaikulu Chidzuma m'boma la Kasungu.

Malingana ndi mneneri wa ofesi ya za umoyo mboma la Kasungu a Isaac Mwavuli, anthu ena am'mudzi ndi omwe anapeza khandali pa thengo lina m'deralo, la Mulungu pa 24 May, ndipo anathamangira nalo pa chipatala chaching'ono cha Anchor Farm, komwe akulisunga kufikila pano.

Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za polisi ya Kasungu Sergeant Miracle Hauli wati amva za nkhaniyi koma apempha nthawi asadalankhulepo zambiri.

Wolemba Raphael Mapira Kasungu

Linga FM Online

Ntchito yootcha makala akuti siifunika kumangochitapo ayi, kamba koti imafunika kukhala ndi chilolezo komanso malo oyene...
25/05/2026

Ntchito yootcha makala akuti siifunika kumangochitapo ayi, kamba koti imafunika kukhala ndi chilolezo komanso malo oyenela, zinthu zomwe zapangitsa kuti bambo wina wa m'boma la Salima, akhale ku ndende kwa miyezi 46 ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga.

Ofalitsa nkhani za apolisi m'boma la Salima Sub Inspector Rabecca Ndiwate ati bwalo la milandu m'bomali lagamula a Gift Zamanemba, komanso a Chikondi Manyowa, kuti akakhale kundende kamba kowapeza olkwa pa mlandu opezeka akulowa nkhalango ya Thuma, kunyamula zikwanje, makasu ndi kudula mitengo yomwe amawotcha makala, popanda chilolezo.

Sergeant Memory Shawa omwe ndi wapolisi ozenga milandu ya boma anauza bwalo Salima First Grade Magistrate kuti 10 May 10 chaka chino, ma ofisala oyang'anira nkhalangoyi anapeza awiriwa akukonza malo oti awotchepo makala.

Opalamulawa anauvomela mlanduwu ndipo anapempha chilango chofewa koma oweluza milandu, Magistrate Imran Phiri anagwirizana ndi mbali ya boma ndipo anawalamula awiriwa kuti akakhale kundende ngati chenjezo kwa ena amalingaliro amtunduwu.

Daniel Philimon, Salima

Linga FM Online

Address

P. O Box 351 Kasungu

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Linga FM Online posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share