
19/07/2025
Apolisi ku Chiponde m'boma la Mangochi amanga banja lina kamba kopezeka ndi mfuti.
Mneneri wa apolisi m'bomali a Amina Tepani Daudi wati awiriwa, a Shukran Maxon ndi mkazi wawo a Sakina Mustapha, onse a zaka 21, awagwira dzulo ku Chiponde, mkaziyu ataba zovala ndipo amabisa m'chikwama momwe anasunga mfutiyo.
A Tepani Daudi ati anthu atamuchita chipikisheni mkaziyo ndipomwe anapeza mfuti yaing'ono ya mtundu wa pistol, ndipo atamutengera kupolisi komwe anawulula kuti ndi ya mamuna wake, Maxon, yemwe anali atathawa.
Iwo ati atagwira mamunayu, anavomera kuti ndi mfutiyi ndi yakedi yomwe anabwera nayo kuchokera ku South Africa, ndipo kafukufuku ali mkati popeza akukayikira kuti mwina awiriwa amafuna kuchita umbanda ndi mfutiyo.
Padakali pano, kuli malipoti akuti anthu a m'mudzi wina m'dera la TA Mtonda ati atola chida choopsa chomwe apolisi ati ndi "gr***de" pachingerezi, chomwe akuganiza kuti chinatayika pa nthawi yomwe ankakagwira ntchito m'derali sabata latha.