BIBLE, BIBLE BASI

BIBLE, BIBLE BASI Ili ndi tsamba lomwe tidziuzana za Mulungu. Maka zimene baibulo limanena koma sitinvetsa. Zolembedwa

15/07/2020

CHIFUNDO CHA MULUNGU

Kodi chifundo tingachifotokoze bwanji? Luka 10:30-37
Mosiyana ndi mlevi, msamaliya sanaone kusiyana kwa pakati pa iye ndi munthu ochitidwa chifwamba. Iye anamuthandiza munthuyu posayembekeZera dipo. Chotero chifundo ndicho kumuthandiza mzako posayembekezera dipo. Ilitu ndilo khalidwe LA Mulungu.
Aefeso 2:4-6
Pamene Ife tinali akufa mu uzimu , Mulungu anatuma Yesu kudzatifera. Palibe chimene tikanamupatsa iye pa chifundo chotero. 1petro 1:3
Werenganinso Aroma 9:15-16

Pali chimodzi chokha chimene chingathe kutipanga ife kukhala oyenera kulandira chifundochi. Chimenechi. Chimenechi chikupezeka pa Luka 1 :50, masalimo 25:10.

15/07/2020

CHIFUNDO CHA MULUNGU

Kodi chifundo tingachifotokoze bwanji? Luka 10:30-37
Mosiyana ndi mlevi, msamaliya sanaone kusiyana kwa pakati pa iye ndi munthu ochitidwa chifwamba. Iye anamuthandiza munthuyu posayembekeZera dipo. Chotero chifundo ndicho kumuthandiza mzako posayembekezera dipo. Ilitu ndilo khalidwe LA Mulungu.
Aefeso 2:4-6
Pamene Ife tinali akufa mu uzimu , Mulungu anatuma Yesu kudzatifera. Palibe chimene tikanamupatsa iye pa chifundo chotero. 1petro 1:3
Werenganinso Aroma 9:15-16

Pali chimodzi chokha chimene chingathe kutipanga ife kukhala oyenera kulandira chifundochi. Chimenechi. Chimenechi chikupezeka pa Luka 1 :50, masalimo 25:10.

Odala ndi iwo akunva mau ndi kuwachita

05/07/2020

Kuwala

Kuwala ndi chinthu chofunika kwambiri pano padziko. Kuwala kumapanga zinthu kuti zizitha kuoneka. Kuwala kumathamanga mtunda okwana 300 000 km pa sekondi imodzi. Ndipo kuwala kwa dzuwa, lomwe lili pa mtunda wa 150 miliyoni kilomitazi kumatenga maminitsi 8 kuti kufike pano pa dziko. Ndi chinthu chodabwitsa kuti Mulungu anatikonda ife natipatsa zinthu angati zimenezi. Yesu akuti:

Ndadza Ine kuunika ku dziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima. Yohane 8: 46

Pambali pa kuwala kwa dziko, Yesu anadza kudzatipatsanso kuwala kwa uzimu.

Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako, yohane 12:35

Ndizosatheka munthu kukhala wa Yesu koma ndikumayenda mu mdima. Inde, munthu oyenda mu mdima ndi kosavuta kulumidwa ndi njoka. Munthu osakhala ndi Yesu ndikosavuta kulumidwa ndi njoka, satana. Chotero tiyeni mthawi zonse tikhale anthu oyenda mkuwala.

AMEN

02/07/2020

Hi all. Ndakunyadirani tiyeni tipilize kumawerenga maphunzirowa ndi othandiza. Sakulembedwa potengela maganizo a anthu kapena mpingo koma bible basi. Good night all

01/07/2020

KUBWERANSO KWA YESU KHRISTU

Chiphunzitso cha kubweranso kwa Khristu ndicho tsinde lenieni la malemba oyera. Kuchokera pamene makoli athu anachimwa my Edeni , anthu akhala akuyembekeza tsiku limene mphanvu yamdani wathu satana mdierekezi idzathetsedwe. Inde tsiku linens tidapatsidwenso Edeni watsopano.

Yoh 14:1-3. Yesu Khristu adzabweranso.
Mach 1:9-11. Iye adzabwera monga momwe anapitila.
Chiv 1:7. Diso lililonse lidzamuona.
Mateyu 24:30. Adzabwera ndi ulemelero komanso mphanvu.
Mateyu 25:31. Adzabwera ndi khamu LA angelo.
Chiv 6:15-17. Oipa adzalakalaka kubisala kuopa ulemelero wa Yesu.
Yeremiya 25:31. Adzabwera ndi miyandamiyanda ya Angelo.
Yeremiya 25:30-33. Oipa adzakanthidwa.
Luka 17:26-30. Adzabwera my nthawi imene anthu sakuyembekezera. Monga momwe zinalili nthawi ya Nowa.
1 Akor 15:51-53. Oyera adzasanduka osafa.
Luka 21:34-36. Tikonzekere kudza kwake.

Zotsatira za kudza kwake

Yesaya 2:17-22. Dziko lidzagwedezeka
Chiv 6:14-17. Mapiri ndi zilumba zidzasuntha
Yesaya 24:1,3-6. Dziko lidzasanduka bwinja
Chiv 20:1-3. Satana adzamangidwa
Chiv 20:4-6 Ochimwa adzauka patadutsa zaka chikwi chibwelereni Yesu kachiwirika.
Chiv 20:7-8. Satana adzamasulidwa akadzauka ochimwa
Chiv 20:9-10. Satana ndi anthu ochimwa adzathedwa limodzi.
2 Petrol 3:7-13. Moto omwe udzanyeketse satana ndi Angelo ake komanso anthu ochimwa, udzakhala pa nthawi yomweyo ukukonzanso dziko lino.

Dziko latsopano

Masalimo 115:16. Dziko lokonzedwa mwatsopanoli lidapatsidwa kwa ana a anthu
Yesaya 51:3. Dzikoli lidzafanana ndi momwe analili Edeni
Yesaya 33:24. Sikudzakhala asing'anga, zipatala kapena mapanado popeza matenda idzakhala mbiri yakale
Yesaya 66:22-23. Tidzapitiliza kupembedza Mulungu.
Chiv 21:1-2 Likulu lake lidzachita kutsika kuchoka kumwamba.
Chiv 21:18 Udzakhala mzinda was golide
Yesaya 30:26. Kudzakhala kowala kuposa madzuwa 7 kuphatikiza.
Chiv 22:1-2. Kudzakhala mtengo wa Moyo uja unali mu Edeni

30/06/2020

Masiku atatu mmanda 3

Ndipo tsiku lotsatira (lachitatu/ Wednesday), Yesu anapachikidwa pa mtanda. Ndipo nthawi ya 3 koloko iye anapeleka mzimu wake, kukwangula onse. Iyi inali nthawi imene msembe inali kupelekedwa ku kachisi. Ndipo anaikidwa mmanda madzulo pamene dzuwa linali kulowa (6 koloko). Ayuda anayesetsa kumuika mmanda dzuwa lisanalowe chifukwa tsiku lotsatira linali tsiku la chikondwelero cha mkate opanda chotupitsa, inde tsiku la sabata lalikulu. Pa tsikuli anthu sanali kuloledwa kugwira ntchito iliyonse. Sabata lalikuli lomwe ndi pa 15 Nisani linali pa tsiku lachinai (Thursday).

Pa tsiku lotsatira (friday) azimai anapita kukagula mafuta onunkhira komanso kukonza zina ndi zina zokonzekera kudzodza mtembo wa Yesu. Tsiku ilinso ndi lomwe amsembe anapempha mfumu kuti iike alonda ku manda poopa kuti ophunzira angabe mtembo wa Yesu ndikumalengeza kuti wauka. (Mateyu 27:62-66). tsiku lotsatira lomwe akunena apa ndi lachisanu litatha sabata lalikulu. Tsikulinso linali tsiku lokonzekera sabata la pamlungu (Saturday). Ndipo pa tsiku lasabata anthu anapuma ku ntchito zawo. Koma sande mmawa amai aja analawira kumanda kukadzodza mtembo wa Yesu ndipo anapeza atauka.

Baibulo limati Yesu anauka pa tsiku loyàmba la pa mlungu. Tikuyenera kuzindikira kuti mu baibulo tsiku limayamba ndi mdima. Kunthauza kuti tsiku la sande lomwe Yesu anauka linayamba pakulowa pa dzuwa tsiku lasabata (Saturday). Chotero Yesu anauka mmanda litangodutsa sabata. Ndipo izi zikutanthauza kuti Yesu anakhala mmanda ndendende masiku atatu usana ndi usiku. Kapena kuti maola 72 monganso momwe anakhalira Yona.

Ichi ndicho chizindikiro cha Yona chimene Yesu anapeleka pa Mateyu 12:40.

Chiphunzitso chakuti Yesu anapachikidwa lachisanu ndi kuuka sande sichiphunzitso cha baibuĺo ayi. Komano chisokonekero chomwe chinachitika pamene choonađi cha baibulo chinasokonekera mu zaka 300 Yesu atapita kumwamba. Imeneyi inali nthawi yomwe boma linaphatiķiza chikunja ndi chikhristu ndikupanga mpingo watsopano.

30/06/2020

masiku atatu part 2

Ndipo tsiku lachisanu Yesu anafika ku Yerusaĺemu atakwera pa bulu.Tsiku limeneli ndi lija iye anathamangitsanso amalonda mkachisi komanso anayamba kuphunzitsa ndi mphanvu komanso ulamuliro.

Tikuyenera kuzindikira kuti masiku otsatira kuchokera tsiku lija Yesu analowa mu Yerusalemu komanso kukwapula ogulitsa malonda anali ofunika kwambiri mu mbiri ya msembe chifukwa anali kugwirizana kwambiri ndi zomwe ziñalembedwa pa Exodo 12:3-8.

Awa anali masiku anai amene kalero aisraeli anali kupatula ana a nkhosa a chaka chimodzi oti adzaphedwe pa 14 mwezi umenewu wa Nisani. Mukawerenga bwinobwino Mateyu 23 muona kuti Yesu akudzudzula kwambiri atsogoleri chifukwa chakukakamila ziphunzitso za makolo awo mmalo motsata chilungamo. Ndipo kopitilira ka 8 Yesu wakhala akunena kuti tsoka alembi ndi afalisi.

Ndipo mu nthawi yokhayokhayi, ansembe akumufufuza Yesu kuti amupezere chifukwa koma sichikupezeka. Ukutu kunali kufufuza komwe kuja kwalembedwa mu chipangano chakale.

Ndipo pa 13 mwezi wa Nisani Yesu ndi ophunzila ake anakonza mgonero. Umenewu machitidwe ake anasiyana pang'ono ndi mgonero uja umene unadyedwa panthawi ya ķutuĺuka mu Igupto. Exodo 12:5-11. Chakudya ichi cha p***a ana a Israeli anali kudya mwachangu komanso atadzimangila nchiuno. Iwo anali kudya atavala nsapato. Inde, anali kudyanso zitsamba zowawa pophatikiza ku nyama zophedwazo.

Mgonero wa Yesu unali osiyana. Iye sanapange mopupuluma ayi. Anadya atavuĺa nsapato komanso kusambitsana mapazi. Inde, iwo sanadye nyama komanso zitsamba zowawa. Mmalo mwake anadya mkate namwa vinyo. Chotero tikhoza kunena monenetsa kuti mgonero wa ambuye siunali ofana mmachitidwe ndi chakudya cha p***a ayi. Numeri 33:3.

Yesu anagwidwa mmunda wa Getsemani usiku wa lachiwiri, Tuesday ndikutengedwera kwa anthu osiyanasiyana amaudindo kuphatikizapo wankulu wa msembe. Inde uku kunali ngati kufufuza komaliza kuti awone ngatidi iye anali oyenera kukhala msembe ya p***a. Ndipo anapezeka opanda chilema.

Ndipo tsiku lotsatira (lachitatu...

30/06/2020

Masiku atatu m'manda

Pakuti monga Yona anali mmimba mwa cinsomba masiku atatu ndi usiku wace, chomwecho mwana wa munthu adzakhala mu mtima mwa dziko masiku atatu ndi usiku wache. Mateyu 12:40.

Yesu ananena monenetsa kuti adzakhala m'manda masiku atatu ndi usiku wache. Mabaibulo achingelezi amanena monveka bwino kuti iye adzakhala mumtima wa dziko usana utatu komanso usiku utatu. Iye ananena mwachinvekele, mosalambalala, ndiponso mosazungulira. Usana utatu komanso usiku utatu.

Masiku ano anthu timanena kuti Yesu anamwalira pa tsiku lomwe limatchedwa lachisanu nauka sande. Komano ngati iye anamwaliradi pa fulaide nauka sande, ndiye kuti mau omwe ananena pa vesi lapamwambali sanali olondola ayi chifukwa usiku weniweni ndi umodzi wapakati pa lachisanu ndi pachiweru. Nawo usana weniweni unali wa pachiweru basi. Kodi pamenepa vuto lilipati?

Musabata lomaliza isanafike p***a, Yesu anachoka ku Galileya kupita ķu malire a Yudeya kumusi kwa Yolodani (Mateyu 19:1). Ndipo khamu la anthu linamutsata. Ndipo mkati mwa njira iye anawaitana ophunzira ake pambali nawauza kuti akakafika ku Yerusalemu iye akaphedwa popachikidwa (Mateyu 20:18-19). Njira yochoka ku Galileya kupita ku Yerusalemu inali kudutsa ku Yeriko. Ndipo kuchoka ku Yeriko kufika ku Yerusalemu ndi mtunda wa makilomita odutsa pàng'ono 20. Komano ndi ulendo ovuta chifukwa Yeriko alikumusi pamene Yerusalemu ndi kumtunda. Ulendowu unali otopetsa ngati kukwera phiri. Ku Yerikoku Yesu anachiza osaona awiri.

Malingana ndi kafukufuku wa malemba, zochitika za ku Yerikozi zinachitika pa tsiku lomwe pachichewa timalitcha lachinai (Thurday).

Ndipo tsiku lachisanu Yesu anafika ku Yerusaĺemu atakwera pa bulu.Tsiku limeneli ndi lija iye anathamangitsanso amalonda mkachisi komanso anayamba kuphunzitsa ndi mphanvu komanso ulamuliro.

Ikupitilira.....

29/06/2020

Kupitilira kuchokera post yammbuyo

Mateyu 2 :1-2
1Ndipo pa kubadwa kwace kwa Yesu m'Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,2nati, Ali kuti amene anabadwa Mfumu ya Ayuda? cifukwa tinaona nyenyezi yace kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.

Mukawerenga mwachidwi mauwa, muona kuti iwo anadza Yesu atabadwa kale. Ndipo atafika Ku Yerusalemu anayamba kumufufuza komwe anabadwira. Zimenezi zinakawafikitsa mpaka Ku nyumba ya Herodi mfumu. Zimenezi zikutanthauza kuti iwo sanafike tsiku la kubadwa Yesu.

Mateyu 2:11
11Ndipo pofika ku nyumba anaona kamwanako ndi Mariya amace, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula cuma cao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure.

Inde iwo sanapeze khanda mu chodyetsera ng'ombe ayi. Koma kamwana Kali ndi mai ake Maria Ku nyumba. Izi zikunthauza kuti Yesu atabadwa, Yosefe ndi Maria anakhala Kaye Ku Betrehemu kwa kanthawi. Ndipo pamene anzeru a kummawa anafika kwa Herodi anamuwuza Herodiyu tsiku komwe iwo anaona nyenyezi (vesi 7).

Ndipo chifukwa cha msanje Herod anapha ana onse oyambira zaka ziwiri. Mu njira ina zikhoza kutheka kuti pamene anzeru a kummawa ankafika kwa Yesu panali patadutsa nthawi yaitali chibadwireni Yesuyu.

Nyenyezi inaoneka kwa iwo tsiku komwe Yesu anabadwa. Nthawiyi iwo anali Ku mmawa (mwina Ku Babulo). Tsiku limeneli ndi limene anayamba ulendo wao wapangamira kapena akavalo(horse). Anayenda chimodzimodzi kuchokera dziko lakunja ngati Burundi kudza kuno.

29/06/2020

ANZERU A KUM'MAWA

Kodi anzeru a kummawa anali Ndani? Nanga analipo angati? Kodi anabwera liti kudzamuona Yesu? Nanga baibulo limati chani za iwo?

Kodi anzeru a kummawa analipo angati?

Baibulo silinakambepo za maina a anthu omwe anali kutchedwa anzeruwa. Inde silinenanso kuti analipo angati. Ndipo chomwe ilo limanena ndicho chakuti anthuwa anabweretsa Mphatso za mitundu itatu pa tsiku lomwe anabwera kudzaona Yesu. Mphatsozi zinali golide, libano komanso mure. Inde palibe paliponse mu baibulo pamene amanena kuti anzeru a kum'mawa analipo atatu. Zikhoza kuthekha kuti anali opitilira atatu. Anthuwa kwao kunali kutali kummawa. Ndipo malo omwe anali kutchedwa kummawa anali madera monga babulo.

Anthuwa pachingerezi anali kutchedwa 'magi' kutanthauza anzeru, aula kapena openduza. Ndipo ndi anthu angati omwewa amene mafumu otchuka monga Farao, Nebukadineza komanso Amedi ndi Aperesi anali kuwagwiritsa ntchito pamene pachitika chododometsa. Iwo anali akatswiri pa nkhani yodziwa za mlengalenga, kutanthauza maloto komanso kuchita zamatsenga.
Nebukadineza anapanga Daniel ndi anzake kukhala mu gulu la anzeru ake (Daniel 2:11,18,24,27). Ndipo Daniel anasankhidwa kukhala mkulu wa anzeruwa Ku Babulo.

Kudza kwa anzeru a kummawa sikunali kudzalambira Yesu monga Mwana wa Mulungu ayi. Pajatu anthuwa anali okhulupilira zakuthambo osati mlengi. Chotero nkosatheka watsenga kulambira Mulungu.

Kodi anzeruwa anabwera usiku omwe Yesu anabadwa?
Nthawi Zambiri maka mu desembala timaona zithunzi zojambula khanda litagonekedwa mu chodyera ng'ombe ndipo anzeru a kummawa atatu atagwada kumpembedza.

Mateyu 2 :1-2
1Ndipo pa kubadwa kwace kwa Yesu m'Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,2nati, Ali kuti amene anabadwa Mfumu ya Ayuda? cifukwa tinaona nyenyezi yace kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.

Mukawerenga mwachidwi mauwa, muona kuti iwo anadza Yesu atabadwa kale. Ndipo atafika Ku Yerusalemu anayamba kumufufuza komwe anabadwira.

Address

Online
Kasungu

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when BIBLE, BIBLE BASI posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category