
15/07/2025
Mkulu wabungwe la Chifukwato cha Achewa Kalonga Sosola wapempha alimi m'boma la Kasungu kuti azionetsetsa kuti akutenga ulimi ngati malonda ndi cholinga choti azipeza phindu lochuluka pa ulimi.
Kalonga Sosola wayankhula izi pomwe bungwe lawo limodzi ndi kampani ya Afri-oils amasayinirana mgwilizano oti alimi a kopaletivi ya Mtukula mdera la Sub TA Kasera mfumu yandodo Kaomba kuti azilima mbewu ya mtedza komanso nyemba.
Pansi pa mgwirizanowu kopaletiviyi yalandira makina opopela madzi pa ulimi wa mthirira ngati njira imodzi yowalimbikitsa kuti ulimi wawo upitililire kupita patsogolo.
Dalitso Odala yemwe ndi mkulu wa kampani ya Afri-oils wamema alimiwa kuti achilimike kulima mbewu zochuluka ponena kuti msika ulipo kale.
Wapampando wa kopaletivi ya Mtuluka Mofatt Nthembwe wati awonetsetsa kuti akulima mbewu zambiri zomwe zithandizira kutukula miyoyo yawo.
Kumbali yosamalira makina omwe alandila ati awonetsetsa kuti akuyika chitetezo chokwanira kuti anthu asabe kapena kuononga.
Mgwilizano omwe asayinirana ndi wazaka khumi ndipo alimi azipanga ulimi wa mtedza komanso nyemba pochita ulimi wamthilira komanso wamvula ndi kumagulitsa ku kampani ya Afri-oils ndipo maanja okwana 10,000 akudera la Kaomba, Kaluluma mwa ena ndiomwe apindule nawo.
Wolemba: Linly Kamanga