26/05/2026
NKHANI ZAMASEWERO ZA KU ULAYA.
📝 Julian Alvarez khumbo lake akufuna atalowera ku timu ya Barcelona. Koma timu yake ya Atletico Madrid ikumugulitsa pa mtengo wosachepera €150m. Izi zipangitsa kuti timu ya Barcelona ilephere kumugula chifukwa mtengo ndi okwera kwambiri.
📝 Sporting Director wa timu ya Barcelona, Deco, ali mdziko la England makamaka mu mzinda wa London kukapanga madongosolo ofuna kutenga katakwe omwetsa zigoli wa timu ya Chelsea, Joao Pedro.
📝 Xabi Alonso akukomza zofuna kuphwasula squad ya Chelsea ncholinga chofuna kubweretsa ena atsopano. Ndipo waika pa msika osewera onse a Chelsea kupatulako osewera asanu okha omwe ndi; Pedro, Tosin, Cucurella, Palmer ndi Enzo.
📝 Timu ya dziko la Ghana yatsimikiza kuti Muhammad Kudus sapezeka nawo mu squad yatimuyi yomwe ikupita ku World Cup mdziko la United States kamba kovulala.
📝 Mphunzitsi wakale wa timu ya Chelsea, Enzo Maresca yemwe wangolembedwa kumene ntchito ku timu ya Manchester City, akukonza zokumana ndi kukambirana ndi Jack Grealish kuti abwerereso ku timu ya Manchester City.
📝 Timu ya Atletico Madrid yakagogoda ku timu ya Barcelona ncholinga chofuna kugulako Marc Casado.
📝 Pali chiyembekezo choti masabata akubwerawa chitsogolo cha milandu yokwana 115 yomwe timu ya Manchester City chidziwika. Matimu onse amu Premier League akuyembekezereka kudziwitsidwa za tsikuli.
📝 Osewera a timu ya PSG, Ousmane Dembele komanso Hakim ayamba zokonzekera limodzi ndi anzawo lero pomwe akhala asakusewera kamba kovulala. Osewerawa akukonzekera kuthambitsana ndi timu ya Arsenal mu ndime yomaliza ya mpikisano wa UEFA Champions League.
📝 Nico Paz akufuna kukhalabe ku timu ya Como season ikubwerayi. Tsopano Real Madrid ndiyomwe yatsala kupanga chiganizo chomutenga katswiriyu kapena ai.
📝 Jose Mourinho wamudziwitsa kale president wa timu ya Real Madrid, Florentino Perez kuti akufuna kuonjezera osewera kutimuyi.
📝 Ndi ma defender awiri okha atimu ya Real Madrid omwe ayitanidwa ndi matimu amayiko akwawo; R