Mtandire Community Radio

Mtandire Community Radio Our vision is to be the most valued, trusted and vibrant radio station that inspires communities.

  Timu ya Laudon Ideas ikuyembekezeka kukumana ndi timu ya Premier League Select lamulungu likudzali pa bwalo la Mwenela...
26/08/2026



Timu ya Laudon Ideas ikuyembekezeka kukumana ndi timu ya Premier League Select lamulungu likudzali pa bwalo la Mwenela mu mzinda wa Lilongwe.

Poyankhulapo za masewerowa a Kelvin Laudon omwe ndi mphunzitsi komanso mwini wa timu ya Laudon Ideas ati akonza masewerowa mdicholinga chofuna kuwakonzekeretsa anyamata ake komanso kuti aphunzirepo zinthu zingapo kuchokera ku timu ya Premier League Select.

"Tikufuna kuti anyamata athu achoke mantha komanso aphunzire maluso osiyanasiyana kuchokera kwa amzawowa monga mudziwa kuti tikusewera ndi timu ya akatswiri kotero tawakonzera masewerowa kuti azichoka mantha" atero a Kelvin.

Awa ndi masewero apaubale opimana mphamvu.

Olemba:Diverson Ndewere
Mtandire Community Radio

   Week 8 Fixture Olemba:Diverson Ndewere Mtandire Community Radio
26/08/2026




Week 8 Fixture

Olemba:Diverson Ndewere
Mtandire Community Radio

  Bernadette mkandawire  osewera wa FCB Nyasa Big Bullets komanso Scochers wanyamuka kupita ku USA mu mzinda wa Californ...
26/08/2026



Bernadette mkandawire osewera wa FCB Nyasa Big Bullets komanso Scochers wanyamuka kupita ku USA mu mzinda wa California kukayetsa mwayi ku timu ya San Diego Wave

Izi zikutsatira ndi kuchita bwino kwa osewerayi komanso Scochers ku mpikitsano wa Womens Africa Cup Of Nation (WAFCON) omwe umachitikira ku Morocco.

Zambili za ulendowu tikupatsirani mmaprogram otsatira.

Olemba:Diverson Ndewere
Mtandire Community Radio

26/08/2026



BANJA LA BAMBO NDI MAYI BREAK KWA MSANJE LIKUNGEZA ZA KUSOWA KWA MWANA WAO LENARD BREAK WAZAKA 22.
WASOWA DZULO MADZULO PA 24 AUGUST NDIPO ENA AKUTI AMUONA KU GULLIVER LERO PA 25 AUGUST
POMWE AMACHOKA ANAVALA TOP YA PINK NDI TROUSER LA YELLOW

MWANAYU AMADWALA NTHENDA YA KUGWA NDENO AMATI AKAGWA MKUBWERELAMO NDE AMANGOTHAWA
AMENE ANGAMUONE ATHA KUIMBA PA 0998592295 OR 0983333228 OR 0994941433 KAPENA ATHA KUKANENA KU POLICE YOMWE ALINAYO PAFUPI

Mvetserani Pulogalamu ya Mwaweruka bwanji pa Mtandire Community madzulo ano kuyambira 5 O'clock ndi muwulutsi Christophe...
26/08/2026

Mvetserani Pulogalamu ya Mwaweruka bwanji pa Mtandire Community madzulo ano kuyambira 5 O'clock ndi muwulutsi Christopher Chunga

26/08/2026

One summit. Countless possibilities.

Plan International Malawi has supported young people to participate in the National Youth Summit, creating opportunities for youth to learn, connect, and amplify their voice

Watch their reflections and hear why meaningful youth participation matters.

 Bungwe la Chess Malawi muno(CHESSAM) lati zonse zakonzedwa bwino pa Mpikisano wa 2026 Malawi Open Chess Championship, w...
26/08/2026



Bungwe la Chess Malawi muno(CHESSAM) lati zonse zakonzedwa bwino pa Mpikisano wa 2026 Malawi Open Chess Championship, womwe uchitike kuyambira pa 28 mpaka 30 Ogasiti ku Linde Hotel ku Mponela, Boma la Dowa. Akuyembekezeka kusewera osewera ochokera m'mayiko osiyanasiyana.

Mlembi wa CHESSAM, a Francisco Mwangupili, ati mpikisano wamakonowu wakopa osewera ochokera ku Zambia, Zimbabwe, Mozambique ndi South Africa, ndipo akuyembekezerabe osewera ena ochokera kudera la ku Africa.

Iye adati mpikisanowu upatsa osewera a ku Malawi mwayi wosewera ndi anthu amphamvu komanso omwe ali ndi maudindo apamwamba pa chess. Izi zithandiza kukweza luso lawo, komanso ma rating awo a padziko lonse lapansi. Cholinga chachikulu ndi kuthandiza Malawi kuti ikhale ndi "International Master" woyamba.

Pa mpikisano wa 2025, Joseph Mwale waku Malawi adapambana m'gulu la Open, pomwe a Linda Dalitso Shaba waku Zimbabwe adapambana m'gulu la akazi.

Olemba: Patrick Kachinjika -Lilongwe
Zithunzi:CHESSAM

  Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalengezeka kuti yalemba ntchito osewera ochokera ku Liberia Sheku Sheriff pa mgwirizano...
26/08/2026



Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalengezeka kuti yalemba ntchito osewera ochokera ku Liberia Sheku Sheriff pa mgwirizano wa zaka ziwiri.

Izi zachitika pamene bungwe la Football Association of Malawi lalengeza za kutsekulira msika wa ogula komanso kugulitsa osewera omwe utsekedwe pa 21 September 2026.

FCB Nyasa big Bullets pansi pa mphunzitsi wake Wedson Nyirenda wasaina osewera oyamba chibwerereni ku timuyi.

Ndipo akuyembekeza kuonjezera osewera ena kuchokera kunja kwa dziko lino komanso komkuno ku malawi.

Olemba:Diverson Ndewere
Mtandire Community Radio

26/08/2026


Mtolankhani wathu Martha Phiri kucheza ndianthu omwe anali pachisangalalo kuti ana awo kapena abale awo alowa chinamwari ku Mtandire mumzinda wa Lilongwe

  Timu ya Silver strikers Ladies yafika mundime ya semifinal ya mpikitsano wa    omwe ukuseweredwa ku Gaberon mdziko la ...
26/08/2026



Timu ya Silver strikers Ladies yafika mundime ya semifinal ya mpikitsano wa omwe ukuseweredwa ku Gaberon mdziko la Botswana.

Silver strikers Ladies yatsiliza pa nambala yachiwiri mu gulu B .

Timuyi ikumana ndi ZESCO NDOLA GIRLS mawa pa 27 August 2026 mu ndime ya semifinal nthawi ya 4pm.

Silver strikers Ladies yalemba mbiri pokhala timu yoyamba kuno kumalawi ya atsikana kufika mu ndime ya semifinal ya mpikitsanowu.

Matimu a ASCENT ACADEMY komanso MTOPWA LADIES akhala akutenga nawo mbali mbuyomu koma amangotulukira mmagulu.

Olemba:Diverson Ndewere
Mtandire Community Radio

Address

Lilongwe

Telephone

+265999138043

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mtandire Community Radio posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category