24/03/2026
DESTINY HELPER
Part 1
"Kodi iwe melina kubwela nthawi zino kusukulu bwanji? Mwina sukulu ukuyitenga ya ambuyako sichocho?
" Pepani sir kuchedwaku sikunali kufuna kwanga kungoti........(asanamalize kuyakhula sir anamudula pakamwa )
" Kunali kufuna kwanga mesa ? Kufuna kunditapa kamwa mesa ?
Sir anafufuma ngati finya ndipo melina anadabwa nao kuti nkhani yake yomweyi paka kumudzazila chochi.ndipo anamugwila kumukokela kati kuti amukwapule.
" Mwanawe zibwezi zomwe ukumapanga zomwe zikumakuchedwesa kuno ndipo apa ndikuomba paka utupe ndipo ukaziuze kuti " eti musandichedweseso.
Melina anayamba kulila yekhayekha mwana nsikana uku azake mukalasi akumuseka ena kumuvela chisoni.
" Kodi mphokosoli bwanji ? (Anafusa m'phunzisi wakulu yemwe amaphuzisa ku fomu 4 )
" Nkhala ngati ndi ku fomu 3 .
Ndipo m'phunzisi wakulu ananyamuka kulowela ku fomu 3 ndipo atafika pa nkhomo la kalasi anagwila kukamwa ataona sir gwebe atapanilila mwana kuli kumukwapula ndipo sir ataona kuti phokokoso lasiya la ana anasiya kumukwapula kaye Melina kuti awone yemwe anayimisa mademo .
" Aaaaaa mr gwebe chikatelo chani ndi mwanayo ? Anafusa m'phunzisi wakulu.) Walakwa chani mwanayo kuti paka mufike pomukwapula chochi?
Melina anali akungolila ndipo nthupi lake mbali yina yinali yitatupikaka Kwambiri mumaziwa kuti azathu akaziwa sachedwa ndipo kulimba kumavuta...........