08/01/2026
Mayi wazaka 38, Esther James, amugamula kukakhala ku ndende zaka zisanu ndi chimodzi kaamba kopezeka olakwa pa mlandu othyola ndi kuba katundu m'nyumba wa ndalama zokwana K149,000.
Bwalo la milandu ku Lilongwe ati linauzidwa kuti mayiyu adapalamula mlanduwu mu April m'chaka cha 2024, ku Area 36 munzinda wa Lilongwe.
Malinga ndi mneneri wa polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, maulendo atatu onse, mayiyu anathyola nyumba ya mayi wina ndikubamo katundu osiyanasiyana monga sugar, mafuta ophikira, zitenje komanso matilesi.
Olemba: Catherine Banda, Lilongwe
copied...