
15/07/2025
Chipwirikiti ku Europe: Achinyamata a ku Africa Akulumikizidwa ndi Ziwawa Mumisewu ku Spain, France ndi UK
Mu mizinda ya ku Spain, France ndi UK, zinthu zakwiyira. Mavuto akuchitika m’misewu pomwe magulu a achinyamata, ambiri ochokera ku North Africa, akuwoneka akuchita zachiwawa monga kuukira anthu, kuwononga katundu ndi kubweretsa mantha kwa nzika.
Zithunzi zomwe zikuyenda pa social media zikuwonetsa kusagwirizana pakati pa alendo ndi nzika, ndipo ambiri akuyamba kufunsa kuti:
Kodi achinyamata a ku Africa akufika ku Europe chifukwa choti akufuna moyo wabwino kapena akuchita izi mwadala?
Kodi mayiko aku Europe akulephera kusamalira alendo awo? Kapena Africa ikulephera kusunga achinyamata ake?
Pa Sunshine Malawi Online Radio tikufufuza mfundo izi:
N’chifukwa chiyani achinyamata a ku Africa akuchita nawo chipwirikiti ku Europe?
Kodi ndale za Europe ndi zomwe zakolezera izi?
Kodi Africa iyenera kutenga phunziro lanji?
Mverani pa www.sunshinemalawi.com kuti mumve zambiri pa nkhaniyi.