13/05/2026
KUSAMVANA PA BWALO LA JOYCE CHITSURO STADIUM.
Kusamvana komwe kunalipo pakati pa bungwe la Southern region football association ndi SULOM tsopano kwatha, Malingana ndi ma report omwe tapeza Kusamvanaku kunabwela kamba koti Bungwe la SULOM linaika masewelo a FDH PREMIERSHIP pa tsiku lomwe a bungwe la Southern region football association anaikaso Launch ya league yawo ya Finca Southern region Premier league pa tsiku la Sunday pa 17 May 2026.
Ma report akuti Southern region football association ndiyomwe inayamba kuika masewela ake a launch pakati pa Mwanza Stars ndi Nyasa Big Bullets reserve. Pomwe SULOM yalengezetsa Monday week yomwe ino kuti masewelo a pakati pa Nyasa Big Bullets ndi Red Lions akakhala pa Stadium Yi tsiku lomwelo.
Panachitika zokambilana pakati pa SULOM ndi Southern region football association ndipo agwilizana kuti Launch ya Finca Southern region football association ikhale ikuchitika pa 24 May 2026.
Zatelemu ndiye kuti Nyasa Big Bullets π Red Lions ikhalapo lamulungu pa 17 May 2026.