Mavuto News Page Line

Mavuto News Page Line Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Mavuto News Page Line, Media/News Company, Lilongwe.

28/04/2022

RUSSIA πŸ‡·πŸ‡Ί πŸ†š Ukraine πŸ‡ΊπŸ‡¦ PANO ZIRIPATI

Tikudziwa ambiri mitima iri m'mwamba kuti mudziwe kuti lero ziripati. Koma tayambira m'mawa kusunzumirako, sitikuonako za nzeru kwenikweni zomwe zachitika lero. Zina mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zachitika lero ndi izi;

1). Nduna yayikulu ya dziko la Sweden πŸ‡ΈπŸ‡ͺ, mayi Magdalena Andersson akana zomwe anthu ena m'dzikomo akufuna kuti dzikolo lichite chisankho cha referendum, kuti anthu asankhe ngati kuli koyenera kuti dzikolo lilowe mu mgwirizano wa NATO kapena ayi. Andersson wawuza atorankhani kuti sikoyenera kuti dzikolo lichite kupanga referendum kamba ka ganizo lofuna kulowa NATO, ndipo ati chiganizocho sichovuta kuchipanga, choncho sichikufunika referendum.

2). mayor wa mzinda wa Mariupol a Vadym Boychenko ati anthu pafupifupi 100, 000 omwe atsala mu mzinda wa Mariupol, omwe ambiri a iwo akubisala pa factory ina yopangira zitsuro ya Azovstal steel plant, akhonza kukumana ndi muliri wa matenda monga kolera, kamwanzi ndi ena. Boychenko wati anthuwo omwe atsekeledwa pamalo pomwe pakutentha kuposa 20 Celsius atha kudwala matendawa chifukwa azungulilidwa ndi madzi a umve, chimbudzi (sewage) komanso mitembo ya anthu akufa ziri ponseponse. Mayor-yu wayankhura zimenezi kudzera pa Telegram.

3). Mabomba omwe anaponya asilikali a Russia usiku wathawu awononga chipatala china pa factory ina yopangira zitsuro ya Azovstal steel plant, pomwe anthu wamba komanso asilikali a Ukraine akubisalapo, mu mzinda wa Mariupol, m'dziko la Ukraine. Oleksandr Vershinin yemwe ndi m'modzi mwa asilikali a Ukraine omwe akubisala pamalopo wanena zimenezi kudzera pa YouTube yomwe yawonetsedwa pa TV ya mzindawo. Iye wati anthu avulala komanso kumwalira, ngakhale sananene chiwelengero chawo.

4). Dziko la Ukraine lati likufufuza asilikali 10 a Russia omwe akuwaganizira kuti anapalamula milandu ya nkhondo kudera la Bucha, mu mzinda wa Kyiv m'dzikolo.

5). Bungwe logulitsa mafuta m'dziko la Russia la Gazprom lati Poland ajugurabe mafuta a Russia m'dziko la Germany. Bungweli lati Poland akupitilira kugura mafuta pafupifupi 30 million cubic metres pa tsiku. Dzuro bungweli linasiya kupeleka mafuta ku Poland ndi Bulgaria ponena kuti mayikowo amakana kugura mafuta a Russia pogwiritsa ntchito ndalama ya Rouble.

6). President wa dziko la America a Joe Biden wapempha parliament ya dzikolo kuti litulutse ndalama zina zowonjezera kuti zithandizire Ukraine ndi zida zankhondo, komanso kugwiritsa ntchito pa malamulo oti awonjezere ma sanctions ku dziko la Russia ndi mzika zake.

7). Mtsogoleri wa dziko la Germany a Olaf Scholz ati dziko la Germany likonzeke kuti nthawi iriyonse Russia ikhonza kusiya kupititsa mafuta m'dzikomo.

8) Parliament ya dziko la Germany yaponya vote yomwe yavomereza kuti dzikolo litumize zida za nkhondo za mphavu m'dziko la Ukraine. Dziko la Ukraine lati lakondwa kwambiri kuti aphunguwo avota moteromo.

9) Nduna yayikulu yakale ya dziko la Finland a Alexander Stubb ati pomwe Finland ikuyembekezeka kupeleka chikalata chake chopempha kuti ilowe mu bungwe la NATO mkatikati mwa mwenzi wa May uno, iyembekezere kulandira ziwopsezo zosiyanasiyana kuchokera m'dziko la Russia.

10). Mayiko amu bungwe la European Union (EU πŸ‡ͺπŸ‡Ί) ati agwirana kuti asavomere ganizo la Russia loti mayikowo azigula mafuta aku Russia pogwiritsa ntchito ndalama ya Rouble.

Nanga pali nkhani ya mzeru pamenepa?

05/03/2022

Mutiuzako zotan gyz zokhudza russiu ndi ukrain? πŸ€›πŸ€›πŸ€›πŸ€›πŸ€›

Address

Lilongwe
KASUNGU

Telephone

+265999728162

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mavuto News Page Line posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share