20/04/2025
JONATHAN LEE RICHES.
Uyu ndi munthu odabwitsa okonda milandu kwambiri ndipo anatengerapo ku court company ya GUINNES WORLD RECORDS chufukwa chomupatsa mphoto (award).
Jonathan Lee Riches ndi munthu yemwe anapanga maphunziro azamalamulo (Law).Anabadwa pa 27 December 1976.Iyeyu ndi munthu osamvetsetseka chifukwa chokonda kumangitsa anthu,iyetu sasankha munthu, chingakhale kuti mukucheza naye ndipo m'macheza mwanumo simunamusangalatse sachedwa kukutengerani ku court mpaka mumulipira ndithu, anatchuka koophsa chifukwa chakuti anakwanitsa kudziimira yekha pa milandu yosachepera 3000 ndipo anawina milandu yokwana 2500.Izi zinapereka chidwi kwa anthu ndipo pa chifukwa cha ichi company yomwe imalemba nkhani zopatsa chidwi padziko lapansi yotchedwa Guiness World Records inalemba nkhani yake mpaka kumupatsa mphoto.Mkuluyu analandiradi mphotoyo ngati zabwinobwino, koma pamasiku ochepa, anaitseguliranso mulandu company yi ati polemba nkhani yake iye osadziwa komanso pomupatsa mphoto(award) ngati munthu okonda milandu.Anadziimira yekha ngati lawyer pa mulanduwu ndipo anapambana natchaja ndalama zambirimbiri ngati chindapusa ndipo analandiradi ndalamazi.
Jonathan Lee Riches, mulandu wake oyambilira weniweni omwe anatchuka nawo ndi mulandu omwe ankazenga mayi ake eni eni omubereka, iye anaziimiranso yekha ngati lawyer pa mulanduwu, mulanduwu ankazenga mayi ake kuti sanamusamalire bwino kuyambira umwana wake mpaka kukula, apa mayi ake anafinyidwa koopsa pa cross-examination (mafunso) mu court. Ndipo pakutha pa mulanduwu, Jonathan anapambananso mulanduwu ndipo anatchaja amayi ake omuberekawo ndalama zokwana 20 US Dollars ngati chipepeso.Inde anazengapo milandu anthu osiyanasiyana monga azinzake, aneba ake, azibale ake, fiance wake, apolisi, ma judge, anthu ena osiyanasiyana komanso ma kampani ambiri otchuka, anazengaponso mulandu President Goerge Bush wa ku America.
Jonathan analemera kwambiri chifukwa cholandira zipepeso pa milandu yosiyanasiyana ndipo iye anakhalans