16/02/2024
GDTV news
Chipani cha DPP chamema nzika za dzikolino kuti zikhale tchelu powonetsetsa zina mwa mfundo za ulamuliro wa demokalase kuti aliyense kuphatikizapo adindo azitsatira ponena kuti demokalase yamdzikolino ili pachiopsyezo chachikulu ndipo anadzudzulanso boma la tonse pophwanya ma ufulu awathu angakhalenso atolankhani
Mtsogoleri waaphungu achipanichi mnyumba yamalamulo a Mary Navicha omwe pamodzi ndi akuluakulu ena achipanichi alankhula izi pamsonkhano waatolankhani omwe unachitikira ku golden peacock munzinda wa Lilongwe.
Iwo adzudzulanso Sipikala wanyumba yamalamulo a Catherine Gotani Hara kuti akuikira kumbuyo a Kondwani Nankhumwa kuti akhale mtsogoleri waaphungu otsutsa boma mnyumba yamalamulo ndicholinga choti mbali yotsutsa boma mnyumbayi ikhale yopanda mphavu.
Mwazina apepha boma kuti lithane ndimavuto a njala, kusayenda bwino kwa chuma, kulephera kupeleka ziphatso zaunzika komanso kukwera mtengo kwa ndalama zolipilira maphunziro
Ena mwa akuluakulu a DPP omwe ali pamsonkhanowu ndi Dr Clement Mwale, mlembi wamkulu wachipanichi, Dr George Chaponda, mkulu osungitsa mwambo mchipanichi mnyumba yamalamulo, a Jappie Mhango, a Chimwemwe Chipungu ndi a Christopher Mzomera Ngwira, gavanala wachipanichi kuchigawo chaku mpoto.
GDTV
Friday 16 February 2024
# Grevaxio Mota