MVAMA TV

MVAMA TV Mvama Television is a registered Tv under Nkhoma SYNOD situated in Area 49. The Minister is Reverend Hamilton Yasin Gammah

09/06/2026

Mwambo wa mapemphero (Requim Mass) wosanzikana ndi mzimu wa malemu Inkosi ya Makosi Mpezeni ya chisanu, yaku Zambia uli mkati.

Mfumuyi yomwe dzina lake lenileni ndi David Njengambazo, inamwalira pa 30 May chaka chino ili ndi zaka 75, itakhala pa mpandowu kwa zaka 44.

Thupi lake liikidwa m’manda lero ku nyumba ya chifumu, ya Ephendukeni m’boma la Chipata, Eastern Province, ku Zambia.

Mtsogoleri wadziko la Zambia Hakainde Hichilema, ali nawo pa mwambo umenewu.


A polisi ku Mponela m’boma la Dowa amanga aphunzitsi awiri pa ngala primary school, powaganizira kuti anathandizira ana ...
09/06/2026

A polisi ku Mponela m’boma la Dowa amanga aphunzitsi awiri pa ngala primary school, powaganizira kuti anathandizira ana asukulu kubera mayeso a Standade 8.

Awiriwa, a Hendrina Kachule ndi a Kapindula Kalajere, omwe anapatsidwa ntchito yoyang’anira olemba mayesowa, akuganziridwa kuti anagawira ana a sukulu mapepala okhala ndi mayankho kale.

M’neneri wa polisi ya Mponela MacPatson Msadala, watsimikiza za nkhani imeneyi, pomwe akupitiliza kufufuza zambiri.

Wolemba: Young Andrew Mahiyu


Fodya wolemera ma kilogalamu 51.5 miliyoni wandalama zokwana 107 miliyoni dollars ndiyemwe wagulitsidwa mumiyezi isanu n...
09/06/2026

Fodya wolemera ma kilogalamu 51.5 miliyoni wandalama zokwana 107 miliyoni dollars ndiyemwe wagulitsidwa mumiyezi isanu ndi iwiri pansika wa fodya wa chaka chino.

Izi ndi malinga ndi ripoti lomwe bungwe la To***co Commission latulutsa.

Ripotili lati panthawi yomweyi mu chaka cha 2025,alimi anali atagulitsa fodya olemera makilogalamu 59 miliyoni omwe anapeza ndalama zokwana 143 miliyoni dollars pa ntengo wapakati pa 2.43 dollars pa kilogalamu imodzi.

Ripotili latinso kusachita bwino mu chaka chino kwaza kamba kakuchuluka kwa fodya yemwe anakanidwa pamsika auction.

Wolemba : Chikondi Kuphata


Nduna yazofalitsa nkhani a Shadric Namalomba ali m'dziko la China komwe akukambirana ndi akuluakulu a kampani ya Huawei ...
09/06/2026

Nduna yazofalitsa nkhani a Shadric Namalomba ali m'dziko la China komwe akukambirana ndi akuluakulu a kampani ya Huawei pa ndondomeko yazaka zinayi yopititsa patsogolo ntchito zogawana mauthenga pogwiritsa ntchito njira zamakono za technology.

Pamkumano omwe anachita ndi akuluakulu a kampiniyi a Namalomba anati mapulaniwa akutsamira pa mizati iwiri yomwe ndi kuonesetsa kuti nthambi zonse zaboma zikugwiritsa ntchito njira zamakono zogawana uthenga komanso kulumikiza dziko lonse ndi intaneti yachangu.

Wolemba :Chikondi Kuphata


A Malawi 150 omwe athawa m’chitidwe wa nkhaza wa Xenophobia ku South Africa, tsopano afika m’dziko muno.Nzikazi zafikira...
09/06/2026

A Malawi 150 omwe athawa m’chitidwe wa nkhaza wa Xenophobia ku South Africa, tsopano afika m’dziko muno.

Nzikazi zafikira ku Kamuzu Stadium ku Blantyre, komwe akuziyeza kaye nthenda ya Ebola ndi Covid-19 komanso kuzigayira chakudya.

Unduna woona za ubale wa dziko lino ndi maiko ena ndi nthambi ya boma yoona ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DODMA, mothandizana ndi a polisi, ndi omwe akutsogolera ntchitoyi.

Boma la Malawi ndi lomwe linakonza mayendedwe amenewa kwa nzika zomwe zimafuna kubwelera kumudzi, popewa zipolowe za Xenophobia.

Mu imodzi mwa ma video ali m’munsimu, m’modzi mwa a Malawi omwe afika m’dziko muno, akufotokoza zina mwa nkhanza zomwe amakumana nazo ku South Africa.

Olemba: Young Andrew Mahiyu


09/06/2026

NEWS REVIEW

09/06/2026

Morning Devotion
WIth Rev. H. Y. Gammah

08/06/2026

MU NKHANI ZOMWE ZANGOCHITIKA KUMENE:

Woyendetsa ndege (Pilot) ndi womuthandizira wake (Copilot) amwalira, ndege yomwe amayendetsa itagwa ndikuyaka moto pa airport ina m'dziko la Dominican Republic, pomwe amayetsa kutela mwadzidzidzi.

Ndegeyo ya mtundu wa Jet, yomwe imapita ku Texas m'dziko la America, akuti inaonetsa mavuto angapo itangonyamuka.

Kanema: Al-Jazeera


08/06/2026

SPORTS BOOTH

Bambo wina ku Thyolo wadzipha, atapha mkazi wake ndi mwana wake wa chaka chimodzi, pa zifukwa zomwe sizinadziwikebe.Mali...
08/06/2026

Bambo wina ku Thyolo wadzipha, atapha mkazi wake ndi mwana wake wa chaka chimodzi, pa zifukwa zomwe sizinadziwikebe.

Malinga ndi apolisi aku Thyolo, awiriwa a Pilirani Lunguzi a zaka 36 ndi mkazi wao Zinenani Leornad wa zaka 22, pamodzi ndi mwana wao, anapita kokatola nkhuni loweruka lapitali, komwe zonsezi zinachitikira.

A Lunguzi ankachokera m’mudzi wa Katundu, m’dera la T/A Chimaliro, pomwe mayi Leornard ankachokera m’mudzi wa Muliko, T/A Ngolongoliwa ku Thyolo komweko.


Address

Area 49, Zebra
Lilongwe

Telephone

+265888862699

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when MVAMA TV posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to MVAMA TV:

Share