BrainWave Media

BrainWave Media | Seeing Genius in every Brainwave 🧠 |

Kodi eti munadzifunsapo kuti zinthu zomwe tima deleter pa phone or PC zimapita kuti? 🤔Chabwino mukapanga empty Recycle B...
05/06/2026

Kodi eti munadzifunsapo kuti zinthu zomwe tima deleter pa phone or PC zimapita kuti? 🤔
Chabwino mukapanga empty Recycle Bin kaya ndi Trash, zimakhala zitatheratu? 👀
Tandiuzeni maganizo anu mu comment section 👇
Mwina funsoli Sindili nalo ndekha 😂

26/05/2026

Kodi munagwiritsapo ntchito incognito mode?

Hello guys,Mwaswera Bwanji? Zikomo nonse chifukwa cha support yanu.Lero ndikufuna ndimve maganizo anu pa page .Ndaika an...
25/05/2026

Hello guys,Mwaswera Bwanji? Zikomo nonse chifukwa cha support yanu.
Lero ndikufuna ndimve maganizo anu pa page .
Ndaika anonymous feedback form mu comment section 👇

Feedback yanu ithandiza kuti BrainWave Media ikhale yabwino kwambiri pamene ikupitilira kukula.

24/05/2026

Kodi Mumadziwa chifukwa chomwe phone yanu ili ndi Airplane mode?

M'mbuyomu Nditapanga post video Ya 3D-printed building, ambiri anatsutsa kuti ndizabodza Kulibeko. Incase simunaonere vi...
21/05/2026

M'mbuyomu Nditapanga post video Ya 3D-printed building, ambiri anatsutsa kuti ndizabodza Kulibeko. Incase simunaonere video imeneyi,link ili mu comment section.

Kodi Mukudandaula kuti Phone yanu Ya 128gb ndiyochepa? Koma mukudziwa kuti mu 1956, kukhala ndi storage ya 5MB yokha, un...
19/05/2026

Kodi Mukudandaula kuti Phone yanu Ya 128gb ndiyochepa? Koma mukudziwa kuti mu 1956, kukhala ndi storage ya 5MB yokha, unkayenera kukhala ndi machine olememera pafupifupi 1 ton? Nthawi imeneyi, Picture imodzi yomwe mumatenga pa foni yanu lero, inkafuna Katundu wamkulu ngati Deep freezer.
Chimenechi chinali chiyambi cha ma Hard Drive, Otchedwa IBM 350. Mkati mwake munali ma disk akuluakulu okwana 50.

Koma tamvetsetsani : Ngakhale chinali chachikulu chonchi, chinkasunga data yokwana 5 Megabytes yokha. Lero, 5MB imeneyi ndi Chithunzi chimodzi kapena Ziwiri za HD.
Koma chosangalatsa ndichochititsa chidwi kwambiri ndi mtengo wake wa Hard drive imeneyi. Mzaka zimenezi sikuti mumachigula chinthuchi, koma mumachipanga Rent. Unkayenera kulipira ndalama zopitirira $3,000 pa mwezi, ndalama zomwe masiku ano ndi pafupifupi MK 50 Million pamwezi Kuti ukhale ndi 5MB, Ndiyekuti umayenera kukhala CEO kapena boma kuti ugwiritse ntchito, chifukwa anthu wamba zinali zovuta kukwanitsa kulipila.

Ma engineer a IBM anagwiritsa ntchito Luso la magnet kupanga ma (magnetic disks) omwe ali mu ma Hard Drive mpaka lero. Kuchokera pa 1 tonn ya 5MB mu 1956, mpaka pa MicroSD card ya 1 Terabyte yomwe ili ngati kachikadabo ka chala chanu lero.

Tsiku lina mukamadzadandaula kuti foni yanu kapena hard drive yanu ya 128GB yadzaza, kumbukira kuti mu 1956 unkafunikira Room yonse kuti usunge data yofanana ndi imeneyo.
Pangani like, share & comment. Chachikulu Tapangani follow page lino.
🧠

Kusunga ma password osiyanasiyana ndi ntchito yotopetsa kwambiri. Ndipo anthu ambiri timangosankha njira yosavuta; kugwi...
18/05/2026

Kusunga ma password osiyanasiyana ndi ntchito yotopetsa kwambiri. Ndipo anthu ambiri timangosankha njira yosavuta; kugwiritsa ntchito password imodzi paliponse. Zimasunga nthawi, koma masiku ano imeneyi ndi imodzi mwa njira zosavuta zomwe ma hacker amagwiritsa ntchito kuti apeze information yanu pa internet.Apa sindikungokamba za Facebook yokha, ndikukamba za ma email anu, ndalama zanu, ndi ma account anu onse ofunika. Ndipo zonsezi zingathe kuchitika mu ma minutes ochepa chabe.

Tangoganizani kuti password yanu yomwe mumakonda kwambiri mwaika pa website monga football live scores kapena website ina iliyonse yosafunika kwambiri. Tsiku lina website imeneyo ikapangidwa leak, email ndi password yanu zimatha kukhala poyera. Ma hacker amatenga information imeneyi n’kuipatsa ma robot omwe amatchedwa Spam Bots kapena Credential Bots. Ntchito ya ma bot amenewa ndi kungoyesa email ndi password yanu pa ma website ambiri kwambiri mu nthawi yochepa.
Amayesa pa Gmail, Facebook, PayPal, Netflix, YouTube ndi ma account ena ambiri.

Tsoka limabwera apa,Ngati password yomweyo yatsegula ngakhale account imodzi yokha ngati Gmail yanu, ndiye kuti hacker amatha kulowa mu email yanu n’kudina “Forgot Password” pa ma account anu ena onse.
Password yopangira reset imabwera mu email yomwe iye ali nayo kale. Apa ndiye amatha kutenga control ya ma social media accounts anu kapena ma account ena ofunika.
Iyi ndi imodzi mwa njira zazikulu zomwe anthu ambiri amabetsera ma account awo pa internet masiku ano.

Koma inu ngati Dolo amene munasankha kupanga follow BrainWave Media 😌🔥, n**i njira zomwe zingazakupulumutseni tsiku lina:

Choyamba,Gwiritsani ntchito password yosiyana pa account iliyonse yofunika.
Chachiwiri,Gwiritsani ntchito Password Managers ngati kapena . Awa ndima Password manager odalirika.
Chachitatu , pangani Activate 2-Factor Authentication (2FA) pa ma account anu onse ofunika. 2FA imathandiza kuti ngakhale hacker atadziwa password yanu, asalowe mosavuta chifukwa account imafuna verification ina.

Koma ndikufuna ndikufunseni,Kodi ndi ma website angati omwe munapangako register ndi email yanu koma simunapange delete account mpaka lero? 👀😂Kodi ma website amenewo Data itapangidwa leak lero mukuganiza kuti muli Safe?

18/05/2026

CHENJEZO LOFUNIKA ⚠️

Nthawi zonse mukapita kukapanga photocopy ya *National ID*, khalani maso ndipo musasiye copy iliyonse kumeneko, ngakhale yomwe yawonongeka kapena yalakwika.

Chifukwa anthu ena akugwiritsa ntchito ma photocopy amenewa kulembetsa ma SIM card m’dzina lanu, kenako kugulitsa kwa achifwamba kuti azigwiritsa ntchito pochita zinthu zaumbanda.

Chonde dziwitsani abale ndi anzanu kuti asamale kwambiri pa nkhani imeneyi. Anthu ambiri akulowa m’mavuto chifukwa cha kusasamala.

Abale ndi alongo,tiyeni tikhale osamala.
Al-huda Islamic TV

16/05/2026

Kodi Munafunapo mutamva fungo la chinachake pa video yomwe mumaonera pa social media pano?

Address

Capetown
Lilongwe

Telephone

+265995371612

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when BrainWave Media posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to BrainWave Media:

Share