11/03/2026
Timu ya Barcelona yomwe ikutsogola mu ligi yaku Spain, Laliga yalephera kungonjetsa New Castle United yaku England mu UEFA Champions League pamasewero omwe adali pa St James Park usiku wathawu.
Newcastle United idatsogola mu mphindi 86 kudzera mwa Harvey Barnes ndipo Barcelona idadalira penate yomwe adagoletsa Lamine Yamal pa 90+6.
Matimuwa abwerezana sabata ya mawa ku Spain pabwalo la Camp Nou ndipo wazigoli zambiri adzafika mundime ya matimu 8.
Mumasewero ena Tottenham HotSpurs yagonja 5-2 ndi Atletico Madrid, Atalanta yagonja 6-1 ndi Bayern Munich
Lero masewero apitilira pamene Chelsea isewere ndi PSG, Arsenal ndi Bayern Leverkusen pamene Bodo ndi Sporting FC.
NOB- Radio 11/3/26