
22/03/2025
Mfuti ndi zipolopolo 207 zapezeka ndi Youngstone Kaunda ku Nanthenje mzinda wa Lilongwe.
Izi zili malingana ndi Inspector Hastings Chigalu yemwe ndi mneneri wa apolisi ya Lilongwe.
A Chigalu ati amanga Kaunda atalandira dandaulo pa zomwe iye amachita ndi mfutiyi usiku monga kuwombera m'mwamba ndi kuopsheza makolo ena omwe amati ana awo amakamubera mbatata m'munda mwake.
Momwe zimachitika izi, ndikuti Kaunda ali ndi mlandu wina okhapa munthu ndipo adali akuthawathawa. Iye amachokera m'mudzi Reuben, kwa Kalumbu m'bomali ndipo akhala akukaonekera ku bwalo posachedwapa.
Olemba : Sammey Saulos